Amuna 6 awakwidzinga ataba katundu wa 10 miliyoni kwacha

Advertisement
six men arrested over theft of various items in Lilongwe

Apolisi mu  mzinda wa Lilongwe  amanga amuna asanu ndi m’ modzi chifukwa choba matumba a 78 a mtedza, akina osokera ndi ma sikelo oyezela okwana asanu, zonse za ndalama  zokwana 10.8  miliyoni  kwacha

Malingana ndi mneneli wa apolisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu, mbavazi zidamanga mulonda wa  pa nyumba yosungilamo katundu wa  mayi wina ochita malonda  kwa Njewa ndi kunyamulira katunduyu mu galimoto ya mtundu wa lorry  ya matani 15 mu usiku wa pa 13 febuluwale chaka chino

A Chigalu atsimikiza kuti akusunga a Cosmas Kambale a zaka 26, Lotesi Chakula 31 , Dalitso Mponda 35, Senadi Kasitomu 37, a Robert Kasimu ndi a Chisomo Kajawa a zaka 26.

A Chigalu  ati mu kafukufuku wawo ndi amuna oganizilidwawa, apolisi anatengeledwa ku malo osiyanasina komwe akwanitsa kupeza matumba a Mtedza okwana khumi ndi awiri okha (12) ndipo ati kafukufuku apitilira kuti agwire ena mwa akubawo komanso kupeza katundu otsalayo.

Advertisement