Dalayivala wina waliyatsa liwiro nkusiya galimoto ndi matumba achamba atazindikira kuti payipa

Advertisement
A vehicle which was abandoned by its driver in Dowa

Apolisi ya Nkhunga m’boma la Nkhotakota, akusakasaka dalayivala wina yemwe ananyamula chamba cha nkhaninkhani mu galimoto yomwe iye amayendetsa ndipo atazindikira kuti apolisi akumutsatira anayimika galimotoyo  pa malo ena mkuliyatsa liwiro la mtondo odooka.

Nkhani yonse ikuti dalayivalayu amayendetsa galimoto ya mtundu wa Minibus (Town Ace) yomwe nambala yake ndi CK 10352 ndipo anthu ena anakayikira galimotoyi kuti inanyamula chamba ndipo apa mkuti galimotoyi imachokera ku Dwangwa kupita ku Dwambazi m’mbali mwa msewu wa M5.

Apa anthu akufuna kwabwino anatsina khutu apolisi pa zankhaniyi cham’ma 10 koloko usiku ndipo apolisi sanazengereze koma kuyitsatira galimotoyo ndipo anakumanizana nayo pa Dema ikulowera ku mlatho wa Dwambazi.

Dalayivalayo atazindikira kuti kwanunkha mphira, iye anayimika galimotoyo mkuthawira pathengo lina. Apa apolisiwo anapita mugalimotoyo ndipo atachita chipikisheni anapezako matumba achamba asanu ndilimodzi (6) aja amalemera makilogalamu okwana 90.

Pakadali pano a Sub Inspector Andrew Kamanga watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati galimotoyi komanso chambachi zikusungidwa ndi apolisiwa.

Advertisement