Anthu ena ayamba kuchita mothilira mbewu zawo ku Karonga

Advertisement
800 hectares Mega farm rehabilitation starts in Mangochi

Anthu okhala m’boma la Karonga m’mudzi mwa Mwangosi mfumu yayikulu Kilipula ayamba kuthilira mbewu zawo m’minda yawo pamene kwakhala  pafupifupi masabata atatu kopanda mvula.

Nelson Manda yemwe ndi ophunzira wapa sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University wauza Malawi24 kuti vuto lakusowa kwa mvula pafupifupi masabata atatu kwapangitsa kuti mbewu ziyambe kuuma m’minda ndipo pofuna kuthana ndi vutoli iye komanso anthu ena ayamba kuthilira mbewu zawo.

Malingana ndi a Manda, iwo ati tsopano athilirapo kawiri m’munda mwawo pofuna kuti mbewu zawo zipulumuke kung’amba yomwe yakhudza madera ochuluka mdziko muno.

M’masiku ochepa chabe apitawo nthambi yoona zanyengo ndikusintha kwa nyengo mdziko muno idalengeza kuti ng’amba ikhala ikupitilira mpaka kufika m’mwezi wa April.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement