Nthambi Yoona za Ngozi zogwa mwadzidzidzi (DoDMA) yomwe ili mu Ofesi ya Mtsogoleri wa Dziko Lino ndi Nduna, yati kuyambila m’mwezi wa October chaka chatha kufika mwezi uno, makhonsolo makumi awiri (20) m’dziko muno akhudzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzi.
Izi zadziwika pamene nthambiyi imapeleka tsatanetsatane wa ngozi zogwa mwadzidzi ndi ntchito yopereka thandizo ku maanja okhudzidwa m’nyengo ino ya mvula ya chaka cha 2023/24.
Malingana ndi nthambiyi, ngozizi ndi monga mphepo yamkuntho, mvula yodza ndi mphepo yamkuntho, madzi osefukira komanso mphenzi (ziphaliwali).
“Makhonsolo makumi awiri (20) m’dziko lino omwe ndi a Balaka, Blantyre District, Chikwawa, Chiradzulu, Dowa, Kasungu District, Lilongwe District, Machinga, Mangochi District, Mulanje, Mchinji, Nkhata-bay, Nkhotakota, Ntcheu, Nsanje, Phalombe, Rumphi, Salima, Thyolo ndi Zomba City akhudzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzi.
“Ndipo Chiwerengero cha maanja okhudzidwa chachoka pa 4,751 kufika pa 4,989,” yatero nthambiyi.
Chiwerengerochi malingana ndi nthambiyi ndi pafupifupi anthu 22,450 ndipo anthu asanu ndi atatu (8) atisiya.
Nthambiyi yatinso mwa anthuwa, asanu (5) atisiya ataombedwa ndi mphenzi pomwe atatu adafa ndi ngozi za madzi osefukira ndipo chiwerengero cha anthu ovulala chidakali pa 46.
Padakali pano, nthambiyi yakwanitsa kupereka chithandizo ku maanja 4,868 (omwe ndi anthu pafupifupi 21,906 komanso 97 pa 100 alionse okhudzidwa).
“Wina mwa katundu komanso zakudya zomwe zaperekedwa kwa okhudzidwa ndi chimanga, nyemba, mabulangete, ziwiya, komanso mapepala ofolelera nyumba mongoyembekezera,” yatero nthambiyi.
Ndipo Nthambiyi yatsimikizila anthu m’dziko muno kuti ntchito yopereka thandizo ipitilira m’maboma onse okhudzidwa.
Nthambiyi yati ipitilira kudziwitsa anthu onse m’dziko muno za ngozi zogwa mwadzidzidzidzi komanso mmene angachepetsere chiopsezo chokhudzidwa ndi ngozizi.