Boma mothandizidwa ndi Bungwe la Global Fund likumanga zipatala zinayi Zing’ono zing’ono Boma la Neno. Zipatalazi zikumangidwa kumadera ovuta kufikirako omwe alikutali kwambiri ndi zipatala za Boma.
Zipatala zomwe zikumangidwazi ndi Gonthi, Godeni, Feremu ndi kambale ndipo zikumangidwa ndi ndalama zosachepera 1 billion Malawi kwacha.
Polakhula ndi Malawi24, Mayi m’modzi ochokera m’mudzi mwa Felemu, Afinesi Felemu, anati ndi okondwa ndi kubwera Kwa chipatalachi chifukwa anali pa mavuto kwambiri ndipo anakali pamavuto pakuti chipatala chi sichinayambe kugwira ntchito koma akamaliza zonse mavuto amakumana nawo akhala mbiri yakale.
“Mwana akadwala kapena munthu wamkulu akadwala timayesesa kupeza njinga yamoto yomwe amatilipilitsa 7000 kupita ndi kubwera kuti tikafike komwe kuli chipatala ndipo ndimavuto ambiri chifukwa anthu kunoko timangokhala ndipo kuti tipeze ndalama ngati imeneyi ndizovuta kwambiri,” anatero a Felemu.
Malingana ndi a Felemu, anthu a kwa Felemu chitukuko cha chipatala chimenechi achilandira mosangalala kwambiri chifukwa chipatala chomwe amapita chili kutali kwambiri pafupifupi ma kilomita 15 ndipo ambiri amakanika kupitako ndiponso ambiri amamwalira munjira.
“Chaka chathachi tinataya ana awiri a banja limodzi tili mu njira kupita nawo kuchipatala chifukwa cha matenda a Malungo,” anatero a Felemu.
Chipatala china chamangidwaso Kwa mfumu Gonthi ndipo polakhula ndi Malawi24, a Maxwell Nyumbu omwe anayimira a Gulupu a Gonthi anati chipatala achilandira kwa Gonthi ndipo ndi anthu osangalala chifukwa mayendedwe opita Ku chipatala mwa magaleta ndi ovuta kwambiri.
“Tili ndi mitsinje imene imadzadza madzi nthawi ya dzinja imene amayi komanso ana amatha kukomokela munjira choncho kubwela Kwa chipatala ichi ndife osangalala kunoko Kwa Gonthi komanso kuthokoza kwambiri a unduna wa za umoyo komanso mtsogoleri wa dziko lino kulingalila mozama kuti madera akumudzi kukhale zipatala zing’onozing’ono,” anatero a Nyumbu.
Mawu ake khansala Joseph Chiphaliwali wa dera la Ligowe komwe kwamangidwa zipatala ziwiri, Felemu ndi Gonthi anayamikira boma kudzera Ku unduna wa za umoyo pamodzi ndi bungwe la Global Fund powabweletsera zipatala ziwiri mu dera lawo zomwe zithandize kwambiri anthu okhala mu derali.
“Kunoko Kuli mavuto kwambiri mavuto osaneneka. Anthu akuno amavutika kuti apite Ku chipatala kunoko anthu akadwala timapita nawo ku Chifunga komwe ndikutali. Pena matenda akakula timapita nawo ku Mwanza koma nthawi zambiri ku Mwanza amatha kutibweza akatizindikila kuti tachokela kuno Ku Neno ndipo amatiuza kuti tipite kuchipatala cha Ku Neno chomwe chili kutali kwambiri ndi kunoko,” anatero a Chiphaliwali.
Omwe anayimira Nduna ya za Umoyo a Matias Joshua omwe ndi wamkulu oyang’ana za kasinthidwe Ka ntchito Ku undunako anati ndi osangalala ndi m’mene ntchito yomanga zipatalazi ikuyendera ndipo ali ndi chiyembekezo kuti pofika mwezi wa June anthu ayamba kulandira thandizo kuzipatalazi.
“M’mene tayendelamu zikuwoneka kuti zinthu zikuyenda. Tikukhulupilira pomatha miyezi iwiri kapena itatu zipatalazi zikhala zonse zatha. Ogwira ntchito talemba kale ndipo kungomaliza tikhala tikutumiza anthu azayambe kugwira ntchito mankhwala so ayamba kufika,” anatero a Joshua.