Mkangano wa malire: Anthu aku Mozambique atchetchaso chimanga cha a Malawi ku Makanjira

Advertisement
Malawi Mozambique

…phungu wadandaulira boma kuthetsa mkangano wa malirewu

Pomwe pali kale chiopsyezo cha njala yadzaoneni chaka chino, apolisi komanso anthu a mdziko la Mozambique, pa 17 January, 2024 komaso usiku wa loweruka lapitali, atchetchaso chimanga cha a Malawi pa mkangano wa malire apakati pa dziko lino ndi lawolo ku Makanjira m’boma la Mangochi.

Tsamba lino lapeza kuti anthu a midzi yaku Mozambique yomwe yachita malire ndi dziko lino, akumapelekezedwa ndi apolisi amdzikolo usiku ndikuyamba kutchetcha chimanga cha nzika za dziko lino ponena kuti malowo ali mdziko lawo ndipo chaka chino chokha, anthuwa apanga chipongwechi kawiri zomwe zikuika aMalawi mdelari pa chiopsyezo cha njala.

Malawi24 yamvetsedwaso kuti anthu a m’mudzi mwa a Chala omwe uli mdziko la Mozambique, usiku wa pa 17 January chaka chino, anapelekezedwa ndi apolisi a mdzikolo ndikuyamba kutchetcha minda ya chimanga ingapo ya anthu a mmudzi mwa Madi ku Makanjira komweko ponena kuti mindayo ili mdziko mwawo ndipo aMalawi sakuyenera kumaitenga ngati yawo ndi kumalimamo.

Kupatula apo, anthuwa akuti usiku wa Loweluka lapitali pa 20 January, 2024, anapelekezedwaso ndi apolisi a mdzikolo ndikukayambaso kutchetcha chimanga chomwe chili m’minda ya anthu a m’mudzi mwa Lukono ku dera lomweli nkhani yake ya malire omwewa.

Aka sikoyamba kuti izi zichitike kamba koti kangapo kose kumapeto kwa chaka chatha, anthuwa anatchetchaso minda ina ingapo ya a Malawi ndipo tikukamba pano akuti zafika poti akuluakulu a m’mudzi mwa a Chala awuza anthu awo kuti asamamweraneso madzi ndi anthu a midzi yaku Malawi yomwe ndi kuphatikizapo: Makunula, Mkopiti, Madi, Lukono, Ngwati, Bonazani ndi ina yambiri.

“Loweruka pa 20 January,2024, atchetchaso chimanga mudzi wa Lukono. Akumayenda ndi apolisi usiku kumatchetcha chimanga cha anthu a ku Malawi. Tikunena pano anthu aku Mozambique  awaletsa kuti asamabwere kumazacheza ku malawi maka kumidzi yomwe akutchetcha chimanga cha anthuyo kuti mwina  anthu omwe akuwatchetchera chimangawo kuti aziwaona akhoza kuwapanga chipongwe. Chiganizo chimenecho achipanga ndi mafumu moti pano anthu a kwa Chala ku Mozambique sakubwera midzi yozungulira yomwe yakhuzidwa ndikutchetcheredwa chimangayo akumangobwera usiku kuzatchetcha chimanga nkumapita amayenda ndi apolisi awo,” watitsina khutu munthu wina.

Munthuyu watiso kucha kwa Lamulungu pa 22 January, 2024, apolisi a mdziko la Mozambique anathamangitsa anthu omwe anakhamukira ku minda yotchetchedwa pomwe amafuna kukadzionera okha malodzawo.

Mkangano wa malire: Anthu aku Mozambique atchetchaso chimanga cha a Malawi ku Makanjira
Anthu omwe akuwaganizira kuti ndi apolisi a ku Mozambique

“Anthu mamawa uno (Sunday) anakhamukira kukaona komwe atchetcha kucha kwa lero ndiye apolisiwa atawaona anthuwo ndi pamene amabwera kuti awabalalitse anthuwo mungathe kuona muzithuzimo mfuti zomwe anyamula. Apolisi aku Mozambique ndiosiyana ndi apolisi aku Malawi. Awawa sakhala ndi teargas akaona kuti pavuta amangoombera straight ndiye anthu ambili sanawayandikire anabwelera,” anawonjezera choncho munthuyo.

Poyankhula ndi tsamba lino za nkhaniyi, phungu wa dera la kumpoto kwa boma la Mangochi a Benedicto Chambo, ati zinthu zafika pa mwana wakana phala ku Makanjira ndipo wati chodandaulitsa kwambiri nchakuti, pomwe aMalawi akukumana ndi mazanga zime amenewa, boma la Malawi silikuonetsa chidwi cheni cheni za nkhaniyi.

A Chambo atiuza kuti kwazaka zingapo tsopano, iwo okhala akupita ku unduna wa zamalo, unduna wa zachitetezo cha mdziko komaso unduna owona za ubale wa dziko lino ndi mayiko ena kupempha kuti boma lilowelerepo pa nkhaniyi nsanga, koma ati pempho lawo linagwera pa mwala, silinaphule kanthu mpaka pano pomwe mkanganowu wafika pa mponda chimera.

“Nkhaniyi ine ndikuidziwa bwino ndipo ndikuyenda nawo limodzi anthuwo. Zotchetchedwa minda ineyo ndikuziona ndipo ndakhala ndikupita ndi kulankhula nawo. Ndayenda mwa adindo onse ofunikira m’boma monga kwa bwana mkubwa wa boma la Mangochi, ku polisi, mkulu wa apolisi amene ndakumana nawo, unduna wa za malo, unduna owona za ubale wa dziko lino ndi mayiko ena, onsewa ndawafikira koma kuti abwere kuno adzatipatse yankho zikuvuta. Anthu kuno akufuna awuzidwe malire awo enieni zomwe boma mpaka pano silinena kuchokera chaka cha 2011.

“Kutchetchedwa kwa chimanga ndi nkhaza chabe za anthu aku Mozambique koma sindikukhulupilira kuti boma la Malawi litabwera ndi kunena malire enieni anthu aku Malawi angamalimbanebe ndi anthu aku Mozambique. Chinaso chomwe chikutipweteka nchakuti boda (border) siyikuyenera kukhala pomwe ili pano, imayenera kukakhala kumalire kwenikweni a dziko lino ndi Mozambique osati pomwe inayikidwa pano,” wadandaula Chambo.

Kusamvana pa nkhani ya malireyi kunayamba zaka zapitazo pomwe boma la Malawi linachita mgwirizano ndi boma la Mozambique pa ntchito yofuna kuwunikaso malire a mayiko awiriwa omwe poyamba anagawidwa mchaka cha 1920 ndipo ntchito yowunikaso malirewa inayambika mu chaka cha 2012.

Anthu ena ati amaganizira kuti panachitika chinyengo chachikulu pa nthawi yowunikaso malirewa kamba koti akuluakulu a dziko la Mozambique analowa mkati mwa dziko la Malawi ndikuika zizindikira za malire (boundary beacons).

Posachedwapa, mfumu yaikulu Makanjira yomwe inabadwa Akib Ali inatiuza kuti ndiyodandaula kuti anthu mdera lake akuzuzidwa ndi apolisi a mdziko la Mozambique pa nkhani ya malireyi ndipo inapempha akuluakulu a boma omwe akuti m’mbuyomu anawalonjeza kuti adzapita kudelari kukalongosora za malirewa, kuti achite machawi ponena kuti zinthu sizili bwino.

Advertisement