Wanjatidwa kamba kogwililira ana atatu a zaka zinayi

Advertisement

Mnyamata wina opanda dambisi wazaka 18 wavekedwa zibangiri ndikusungidwa mkambolimboli ndi apolisi m’boma la Thyolo kaamba komuganizira kuti adagwililira ana akazi atatu a zaka zinayi zakubadwa..

Nkhani yonse ikuti nyamatayu yemwe dzina lake ndi Milwad Stanley adachita zadamazi ndi ana atatuwa dzana pa 17 January cha ku mtsinje wa Namichimba komwe adakumana ndi anawa chakumadzulo.

Mkuluyu adakokera anawa m’munda wachimanga wina ndikuyamba kuwachita zadamazi.

Mnyamata wina wachichepere adamva kusisima m’mundamo zomwe zidamudabwitsa mpaka adalowa m’mundamo kuti akaone.

Apa mpamene adapeza Stanley akuchita zakuluakulu ndi anawo.

Pakadali pano yemwe ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’bomali a Rabecca Kashoti watsimikiza za nkhaniyi.

Mnyamatayu amachokera m’mudzi mwa Chibwana kwa mfumu yaikulu Nchiramwera m’boma lomweri la Thyolo ndipo posachedwapa akaonekera ku bwalo lamilandu pa mlandu ogwililira.

Advertisement