Akuluakulu oyendetsa timu ya Wanderers awachotsa


Zatsimikizika kuti mamembala a bhodi ya timu ya mpira wa miyendo ya Mighty Mukuru Wanderers awachotsa.

Wapampando wa timuyi a Thomson Mpinganjira atsimikiza za nkhaniyi.

Mu chikalata chomwe wasayina ndi mtsogoleriyu chikufotoka kuti izi zadza kamba ka maganizo a akulualuku omwe ndi eni makampani omwe amathandizira kuyendetsa timuyi.

“Kamba ka kusinthidwa kwa adindowa, chilichose choyenera kuti bhodi ichitepo kanthu chikuyenera kupita kwa Roosevelt Mpinganjira yemwe ndi khalapampando mu uphunguwu.

“Mamembala onse omwe achosedwa akuyenera kukaonekera kwa khalapampando wa bhodi kuti pakhale kukonzaso.” mbali imodzi yakufotokozera kwa chikalatachi.

Mighty Mukuru Wanderers ndi timu yomwe yamaliza chaka chonse cha 2023 osatenga chikho chilichose ndipo yemwe anali phunzitsi wamkulu mu timuyi Mr Mark Harrison anasiya ntchito kumapeto a chaka chatha kamba kolephera kutenga chikho.