Kudya thukuta lawo: Oyimba akusimba lokoma; Njuchi, Driemo apakula pakulu

Advertisement

Zoti mwezi wa January umakhala ndi masiku ochuluka zedi, oyimba ambiri siziwakhudza kamba koti bungwe la COSOMA lawaombola powapatsa dipo la thukuta lawo; komatu awiri obadwa m’ma 2000-wa asadabuza achiyamba kale poti ndiomwe atapa phwamwamwa.

Lero Lachitatu, Bungwe la Copyright Society of Malawi (COSOMA) lagawa ndalama zokwana K505 million kwa anthu aluso mdziko muno ndipo mwa ndalamazi, K279 million ndizomwe zigawidwe kwa oyimba nyimbo pomwe olemba ma buku alandira K139 Million ndipo akonzi a kanema osiyanasiyana agawana K87 million.

Pa mwambo omwe unachitikira ku hotela ya Crossroads mu mzinda wa Lilongwe, oyimba okwana 54 aliyese wapatsidwa ndalama zosachepera 1 miliyoni kwacha komaso zosapitilira 5 miliyoni Kwacha potengera chikoka cha nyimbo zawo mchaka cha 2023 chomwe changothachi.

Ena mwa oyimba omwe alandira ndalama zoposera 1 miliyoni kwacha ndi monga; Keturah, Billy Kaunda Ace Jizzy, Beejay, Gwamba, Avokado, Hilco, , Moses Makawa, Nesnes, Joseph Nkasa, Phyzix, Pop Young, Waxy Kay, Guntolah, Henry Czar, DNA, Lawi, Mlaka Maliro, Suffix, Anthony Makondetsa, Ma Blacks, malemu Walycris, malemu Tremour.

Gulu la chiwiri ndi la oyimba omwe alandira ndalama zoposera 2 miliyoni kwacha aliyese, ndipo mu gululi muli oyimba ngati: malemu Atoht Manje, Great Angels Choir, Malinga, Zonke, Dan Lu, Azizi, Jay Jay Cee, Rashley.

Kupatula apo, oyimba ngati Zeze Kingstone, Patience Namadingo, Janta, Wikise, Lucius Banda, Kell Kay, ali m’gulu la oyimba omwe alandira ma 3 miliyoni kwacha aliyese pomwe Gibo Pearson ndi Skeffa Chimoto alandira ma 4 miliyoni kwacha aliyese.

Oyimba awiri achisodzera Eli Njuchi komaso Driemo, ndi omwe alandira moposa anzawo onse pomwe aliyese mwa iwo, walandira ndalama yoposera 5 miliyoni kwacha.

Poyankhula pa mwambowu, Driemo yemwe anabadwa Shaffie Phiri walangiza oyimba omwe sanachite bwino kuti asafooke ndiposo walangiza oyimba anzake onse omwe apeza kanganyase kuti ndalama apezazi apangira chinthu chowoneka.

“Ena alandira zambiri kuposa ena, koma sizikutanthauza kuti amenewo ndi akutha kwambiri kuposa enawo, ayi. Zikungotanthauza kuti panopa itha kukhala nthawi ya wina wake koma kutsogoloku idzakhalaso nthawi ya wina. Zikungofunika kukankha. Penaso ukagwa ndi pomwe umakhala ndi chilimbikitso kuti ulimbikile. Kuchita bwino kwa ena chikuyenera kukhala chilimbikitso osati chiopsezo kwa ena.

“Kwa oyimba anzanga pena zimakhala zochititsa manyazi kuti panopa anthu adziwa kuti talandira chonchi komano pasapezeke kuti palibe chomwe tapanga chowoneka. Ndalama ingachepe bwanji yamba kanthu kakang’ono kena kake. Kaya uyamba chinthu choti chizikubweretsera K1000 pa sabata bola kusiyana nkukagulira chinthu choti ena atha kungokubera lero nkuthera pompo,” watelo Driemo.

Advertisement