Anthu 7 apezeka ndi kachirombo ka Covid-19 ku Nsanje

Advertisement

Pomwe anthu ochuluka anayamba kuiwala za matenda a Covid-19, zadziwika kuti matendawa anakalipo mdziko muno pomwe ku Nsanje akuti anthu asanu ndi awiri (7), apezeka ndi kachirombo koyambitsa matendawa.

Izi ndi malingana ndi a George Mbotwa omwe ndi m’modzi mwa akuluakulu ku ofesi ya zaumoyo m’boma la Nsanje omwe atsimikizira nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno zokhudza nkhaniyi.

Malingana ndi a Mbotwa, anthu asanu ndi awiriwa apezeka ndi kachirombo koyambitsa matenda a Covid-19 kumathero a sabata yomwe yangothayi pomwe anayezedwa potsatira kuonetsa zizindikiro za matendawa.

Tsamba lino lapeza kuti anthu asanu ndi m’modzi (6) mwa omwe akudwala matendawa, apezeka pa chipatala chaching’ono cha Kalemba, pomwe pa chipatala chachikulu cha Nsanje, papezeka munthu odwala matenda a Covid-19 m’modzi.

Pakadali pano, zikumveka kuti ofesi ya zaumoyo m’bomali, yayitanitsa mkumano wa dzidzidzi kuti akuluakulu a zaumoyo m’bomali akakambirane za njira zomwe angatsate pofuna kuthana ndi kufalikira kwa matendawa m’boma lawo.

Matenda a Covid-19 omwe anayambira mdziko la China mchaka cha 2019,  amayambitsidwa ndi kachilombo kotchedwa kolona (coronavirus) ndipo matendawa apha anthu ochuluka mdziko muno komaso maiko ochuluka pa dziko la pansi.

Zina mwa njira zopewera matendawa ndi monga kusamba m’manja ndi sopo pafupifupi, kuvala zozitchinjilizira kukamwa komaso kupewa kuyandikana kapena kukhudzana mwachisawawa ndi anthu odwala matendawa.

Advertisement