Anjatwa kamba kakupha bambo ofuna ogwilira

Advertisement

Ku Monkey-Bay m’boma la Mangochi, abambo awiri ali m’manja mwa apolisi kamba kakupha bambo wina yemwe akuti anamugwira akufuna kugwililira mayi yemwe anali nyumba yake usiku.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Monkey Bay, Sergeant Alice Sichali omwe azindikira abambo awiriwa ngati a Oscar Lungwa a zaka 34 komaso a Uladi Frank a zaka 25 omwe akuganizilidwa kupha a Ishmael Makiyi azaka 32.

Malingana ndi a Sichali, usiku wa Lachinayi sabata imene ikungothayi pa 11 January, 2024 oganizilidwa awiri, anakumanizana ndi a Mikiyi pa malo ena otchedwa Lake Service Beach omwe ali mphepete mwa nyanja ya Malawi ku Monkey Bay komweko.

Pa nthawiyi, a Makiyi akuti anali atalowa munchisakasa momwe ankafuna kugwililira mayi wina yemwe pa nthawiyi anali akugona.

A Lungwa komaso a Frank anafika pa chisakasachi atava kufuwula kopempha thandizo kwa mayiyo ndipo awiriwa atafika anapezadi a Makiyi ali jijilijijili ndipo kenaka anayamba kuwamenya.

Awiriwi anavulaza bambo Makiyi ndi zibonyongo mpaka mkuluyu anali thapsya, zomwe zinachititsa kakasi oganizilidwa awiriwa ndipo posakhalitsa ananyamula bambo oganizilidwa kufuna kugwililirayo ndikukamuponya pa tchire lina ali chikomokele.

Nkhaniyi inakasiyidwa m’manja mwa a polisi kuderako omwe anathamangira kumaloko ndikukatenga bambo Makiyi kupita nawo ku chipatala chaching’omo komweko ndipo kenaka anatumizidwa ku chipatala chachikulu cha Mangochi.

Apolisi ati bambo Makiyi analengezedwa kuti amwalira atangofika nawo pa chipatala cha Mangochi zomwe zinapangitsa kuti apolisi ayambe kusakasaka anthu omwe achita chipomgwecho ndipo pamapeto pake a Lungwa ndi a Frank anamangidwa.

Awiriwa omwe amachokera kudera la mfumu yaikulu Nankumba, akuyembekezeka kukaonekera ku khothi posachedwapa kuti akayankhe mlandu wakupha munthu.

Advertisement