Mbava inatsakamuka kudenga komwe inabisala apolisi atathira utsi wokhetsa misonzi

Advertisement

Apolisi kwa Jenda akusunga mchitokosi njonda ina yazaka 33 zakubadwa yomwe inapezeka itabisala kudenga la sitolo ndipo anachita kuthira utsi wokhetsa misonzi kuti itsakamukeko.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Macfarlen Mseteka, njondayi yomwe dzina lake ndi Alex Tembo inalowa mu sitolomo yotchedwa Chikwendene Distributors Shop. Njondayi ikuba ndalama inapanga phokoso lomwe alonda anamva.

Apolisi atatsinidwa khutu za nkhaniyi ndi alonda, anathamangira pamalopo. Ndipo njondayo itazindikira kuti kwafika mbola inabisala kudengako.

Apa mkuti nthawi ili chamma 1 koloko m’bandakucha. Apa apolisiwo sanachedwe koma kulowa m’nyumbayi ndikuthira utsi okhetsa misonzi zomwe zinapangitsa kuti njondayo ichoke kudengako ndikugwa pansi. Apa anangozindikira ali m’manja mwa apolisi akumukokera ku waya.

Mwazina njondayi inali itakwangwanulamo kale ndalama zokwana 629,150 Kwacha pa nthawi yomwe apolisi amafika pamalopa.

Njondayi imachokera m’mudzi mwa Thom mfumu yayikulu Chisemphere m’boma lomweri la Kasungu ndipo akuyembekezeka kukayankha mlandu wakuba komanso kuthyola nyumba.

Advertisement