Masewero a AFCON awonetsedwa pa kanema wa SuperSport

Advertisement
Morocco players expected to feature at the AFCON

Kampani ya MultiChoice  yatsimikizira anthu  okonda masewero a mpira mdziko muno kuti mpira wa chaka chino wa Africa Cup of Nations (AFCON) ukhala ukuonetsedwa pa kanema wa Super Sport

Chikalatachi chadza pamene masiku apitawo panali nkhawa yoti SuperSport sionetsa masewelowa pakanemayu.

Ndipo malingana ndi kalata yomwe kampaniyi yatulutsa,  masewera onse okwana 52 akhala akuonetsedwa pa kanemayu.

Masewero akalambula bwalo ayamba loweluka likudzali ndipo anyamata a dziko la Ivory Coast adzakhala akugwelulana Mano ndi anyamata a mdziko la Guinea.

Advertisement