Sindikupita ku Wanderers kapena Bullets, sangakwanitse kundilipira – watelo Khuda Myaba

Advertisement
Khuda Myaba Malawian football player

Khuda Myaba yemwe pano alibe timu yomwe akuonetsera ukatswiri wake, watutumutsa gulu pomwe wanena kuti alibe ganizo losewera mu ma timu a Mighty Mukuru Wanderers komanso FCB Nyasa Big Bullets ponena kuti matimu onsewa sangakwanitse kumulipira pa mwezi.

Myaba wauza tsamba lolemba nkhani za masewero la ‘Wa Ganyu’ kuti mphekesera zomwe zikumveka kuti iye akukambirana ndi akuluakulu a timu ya Wanderers komanso Bullets kuti iye alowere kumeneko sizoni ya masewero a mpira ikubwerayi, ndibodza la nkunkhuniza.

Osewerayu yemweso kumapeto a chaka chatha anali nkamwa nkamwa pakuchoka kwake ku timu ya Tishreen yomwe ndi ya mdziko la Syria, wati iye sangasewere matimu a kuno kumpanje ponena kuti palibe timu yomwe amayiona kuti ingakwanitse kumamulipira ndalama zomwe iye amafuna pa mwezi uli onse.

“Ngati akundifuna ndiye kuti akuyenera kumandilipira ndalama za ku America. £1000 [K1.7 miliyoni] ndi ndalama zomwe ndikufuna monga malipiro.

“Ndawaona ochemelera timu ya Wanderers akunena kuti ndikulowa ku timu yawo ngati kuti angakwanitse kundilipira, Ili ndi bodza,” watelo Myaba poyankhula ndi tsamba la Wa Ganyu.

Nkhaniyi yakwiyitsa anthu ambiri okonda masewero a mpira wa miyendo mdziko muno ndipo ena mwa iwo mokwiya alemba m’masamba anchezo kudzudzula osewerayu kuti uku sikuyankhula kwa bwino ponena kuti kwanu nkwanu mthengo mudalaka njoka.

Asanapite ku timu ya Tishreen komwe wakhalako kuyambira mwezi wa August mpaka October, 2023, Myaba amasewelera timu ya Polokwane City ya mdziko la South Africa, ndipo kuno ku mudzi poyamba anali osewera wa timu ya Moyale Barracks asanapite ku timu ya Silver Strikers mchaka cha 2018.

Advertisement