Boma ligayitsa chimanga chomwe linalanda chochokera ku Tanzania

Advertisement
Maize imported from Tanzania

Ngati njira imodzi yofuna kupewera matenda a chimanga omwe agwa mdziko la Tanzania kuyambukira mdziko muno, boma la Malawi lati likagayitsa chimanga chomwe linalanda anthu ena omwe amafuna achilowetse mdziko muno.

Izi zikudza pomwe boma la Malawi kumapeto a chaka chatha linaletsa aliyese kulowetsa m’dziko muno chimanga chochokera mdziko la Tanzania komanso Kenya ati pofuna kupewa matenda a chimanga omwe anagwa madera ochuluka m’mayiko awiriwa.

 Boma litatulutsa chiletsochi, anthu ochita malonda ena amabweletsabe chimanga chochokera m’mayiko oletsedwawa ndipo boma linalowelerapo ndikuyamba kulanda chimangachi chomwe chinakwana ma “metric ton” oposa 30,000 ndipo china mwa chimangachi chikusungidwa mdziko la Tanzania pomwe china akuti chili mdziko mom’muno m’maboma angapo kuphatikizapo Nkhata Bay.

Koma boma la Malawi kudzera ku nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (DoDMA), lati lamvana ndi boma la Tanzania za tsogolo la chimanga chonse chochokera m’dzikolo chomwe chikuyenera kufika kuno ku Malawi.

Mkulu wa nthambi ya DoDMA a Charles Kalemba awuza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno kuti mayiko awiriwa agwirizana kuti chimangachi china chipititsidwe mdziko la South Africa china ku Tanzania konko komwe chikagayitsidwe kuti chikhale ufa omwe utha kuloledwa kulowa mdziko muno.

A Kalemba ati chiganizochi chabwera kamba koti chiletso chomwe chinayikidwa ndi cha chimanga chokha osatiso ufa omwe akufuna upangidwe kuchokera ku chimanga chomwe boma limasungachi.

Mkuluyu watsimikizira a Malawi kuti posachedwapa awadziwitsa za kubwera kwa ufa wa chimanga omwe ukagayitsidwewu ponena kuti akufuna pakhale chilungamo pa nkhaniyi komaso kuchita zinthu poyera.

Advertisement