M’modzi mwa omwe akufuna kudzaimila kudzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wa dziko lino kudzela ku chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Dalitso Kabambe ati iwo alibe maganizo aliwonse ogwirizana ndi mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera monga akumvekera manong’onong’o kuti akufuna kudzayenda limodzi mu masankho a 2025.
Poyankhula mu uthenga wawo wa Chaka Chino pa tsamba lawo la mchezo, a Kabambe omwe analinso gavanala wa Reserve Bank ati iwo ndi membala wa DPP ndipo sanayambe atakumanapo ndi a Chakwera ndipo alibenso lingaliro lililonse lofuna kukumana nawo pa nkhani ya mgwirizano.
Gavanala wa kale wa Bank yayikuluyi watinso akugwetsedwa mphwayi pamene masiku a masankho akuyandikira maka chifukwa cha zolankhula zodanitsa.
“Ndafuna kukudziwitsani anthu nonse okonda ndikutsatila chipani cha DPP ndi a Malawi nonse kuti nkhani zikukambidwa mumatsamba amchezo kuti ndakumana kapena kuti ndakhala ndikukumana ndi a President a dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndibodza la nkunkhuniza lomwe akufalitsa ndi anthu ofuna kuyambanitsa anthu komanso kugawa chipani cha DPP.
“Ine sindinayambe ndakumanapo ndi a President a dziko lino ndipo ndilibe ma plan ena ali onse pa nkhani ina ili yonse yokhudza mgwirizano ndi chipani cha MCP,” a Kabambe atero.
A Kabambe ati iwo adzakhalabe Membala wa DPP motsogozedwa ndi mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika.
A Dalitso Kabambe ndi m’modzi mwa amene anawonetsapo chidwi chokapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa chipani cha DPP ku msonkhano waukulu wa chipanichi.
Koma pakali pano sakumalankhulanso za khumbo lawoli chifukwa zikuonetsa kuti a Mutharika akufuna ayimenso pa mpando womwewu ndipo akuyembekezeka kukapikisana ndi a Kondwani Nankhumwa.