Boma silikugwirizana ndi chipepeso cha K103 miliyoni kwa Brian Banda

Advertisement
Former Lazarus Chakwera spokesperson Brian Banda

Boma kudzera kwa mlangizi wake pa za malamulo lati likukonza zoti likasume kutsutsana ndi chigamulo choti lipeleke ndalama yokwana K103 miliyoni kwa a Brian Banda ngati chipepeso powachotsa ntchito ya mneneri wa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

M’mwezi wa August mchaka cha 2020, a Banda omwe pano akugwira ntchito ngati mtolankhani ku Times Group, analembedwa ntchito ngati munthu oyankhulira mtsogoleri wa dziko lino, a Chakwera ndipo zikuveka kuti mgwirizano wa ntchito wawo unali wa zaka zitatu.

Koma nthawi ya mgwirizano wa ntchitoyi isanathe, boma la Malawi kudzera kwa akuluakulu a ku nyumba ya chifumu, linachotsa a Banda pa ntchito yawoyi ndipo m’malo mwawo munalowa a Anthony Kasunda omwe pa nthawi imeneyo ankagwira ntchito yofalitsa nkhani ku khonsolo ya nzinda wa Blantyre.

Zikumveka kuchotsedwa ntchitoku kunachitika pomwe a Banda anatsanzika bwino bwino ndikunyamuka ulendo opita ku maphunziro a utsogoleri mdziko la China komwe sanakachedwe kwenikweni ndipo atabwelera kuno ku mudzi, sanabweleleso pa ntchito yawo.

Izi zinapangitsa kuti mkuluyu aganize zokamang’ala za ku chotsedwa pa ntchito kwawo ku bwalo la milandu la ”Industrial Relations”.

Iwo anauza bwaloli kuti amaona kuti sanachotsedwe bwino pa ntchito yomwe analembedwa chomcho amafuna kuti apatsidwe chipepeso, ndipo kudzera kwa wachiwiri kwa mkhala pampando wake a Peter Kandulu, bwaloli linagwilizana ndi pempho la a Banda.

Malingana ndi chikalata cha chigamulo chomwe chikusonyeza kuti bwalori linatulutsa pa 22 December chaka chatha, boma likuyenera kupeleka chindapusa cha ndalama yokwana K103 miliyoni kamba kowachotsa a Banda pa ntchito motsutsana ndi mfundo za mgwirizano wa ntchito yawo.

Koma kudzera kwa ofalitsa nkhani za mlangizi wa boma pa nkhani za malamulo (Attorney General), a Emmanuel Loya, boma kudzera kwa mlangizi wakeyuu, likukoza zokapanga apilo (appeal) pa chigamulo chomwe bwalo la Industrial Relations lapeleka pa nkhaniyi.

A Lawyer awuza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno kuti chiganizo chokapanga apilo chadza kamba koti boma likuona kuti pali mfundo zina zomwe sizinaunikidwe bwino pa nkhani yakuchotsedwa ntchito kwa a Banda.

Advertisement