Mtsikana wa zionetsero wapatsidwa ndalama za malemu bambo ake

Advertisement
Kamenya gets payment after vigil at Malawi Government offices

Potsatira zionetsero zomwe mtsikana wina Hendrina Kamenya anachita ku maofesi aboma munzinda wa Lilongwe Lachinayi zokhudza ndalama za chipukuta misozi za malemu bambo lake, lero Lachisanu boma lapeleka ndalamazi.

Mtsikanayu yemwe ndiwochokera m’boma la Mwanza, kuyambira Lachinayi m’mawa anali ku maofesi a boma ku Capital Hill ku Lilongwe komwe anachita m’bindikilo pofuna kukakamiza boma kuti limupatse ndalama za penshoni ya bambo ake omwe anamwalira akugwira ntchito m’boma.

Malipoti akusonyeza kuti bambo ake a Hendrina anamwalira akugwira ntchito ku nthambi yoyag’anira ndende ndipo ndalama za peshoni zawo zimayenera kupelekedwa zaka zitatu zapitazo koma sizinachitike zomwe zinakwiyitsa mtsikanayu pamodzi ndi azibale ake.

Mtsikanayu akuti wakhala akulephera kupitiliza maphunziro ake pa sukulu yaukachenjede ya Malawi University of Applied Sciences (MUBAS) kamba kosowa ndalama zolipilira fizi ndipo anthu ochuluka omwe anaona ndi kumva nkhani yake kudzera pa masamba anchezo, anakhudzidwa kwambiri.

Ena mwa akuluakulu aboma omwe anakhudzidwa ndi nkhani ya Hendrina ndi mlembi wamkulu mu ofesi yamtsogoleri ndi nduna zake a Colleen Zamba omwe analonjeza kuti amuthandiza ndipo analamura kuti ndalamazi zipelekedwa lero dzuwa lisanalowe zomwe zachitikadi.

Nawo mayi Mary Thom Navicha, omwe ndi mkulu woyang’anira amai mchipani cha DPP, anakhudzidwa ndi nkhaniyi ndipo kuyambira Lachinayi kufikira lero Lachisanu pomwe boma lapeleka ndalamayi, akhala ali limodzi ndi msungwanayu, kumulimbikitsa kuti anatenga njira yabwino ndipo chilungamo chikuyenera kuoneka.

Advertisement