Mwafwa tafwa! ankhonya athu awiri agwebedwa ku Tanzania

Advertisement
Malawian boxer Limbani Lano

Inde chakachi achilowa nawo komatu achilowa nkhope zawo zitatupa fufufuu ngati mandazi. Wilson Masamba komanso Limbani Lano omwe kwathu kuno timawati anamatetule azigogodo, awona chidameta nkhanga mpala ku Tanzania komwe agwebedwa ngati mawa kulibe mpaka m’modziyo anachita kuthawa mu ling’i kuwopa kuphedwa ndi dzibonyongo.

Masamba komaso Lano omwe mu chiyankhulo chaku masewero othidzimulanawa amatchulidwa kuti ma “Light-heavyweight boxer”, anali mdziko la Tanzania komwe anakakhala nawo pa masewero omenyana pokondwelera chaka chatsopano.

Pa masewerowa omwe anakozedwa ndi kampani yolimbikitsa masewero a nkhonya ya Mafia Boxing Promotion ndipo inachitikira pa bwalo la masewero la Mkwakwani ku Tanga mdziko la Tanzania, Lano anatidzimulana ndi Abdallah Paziwapazi pamene Masamba wagonja kwa Richard Mtagi.

Oyamba kubandulidwa ndi zibakera za moto Lolemba pa 1 January, 2024, anali Lano yemwe anayesetsa mpaka anakwanitsa kusewera ndime zonse koma poti atambala awiri salira khola limodzi, Paziwapazi ndi yemwe anapambana nkhonyayi kudzera panjira ya ma “points”.

Poyankhula ndi nyumba ina yowulutsira mawu mdziko muno, Lano anadandaula kuti oyimbira ndi omwe zapangitsa kuti iye agonje pa masewerowa.

“Ndinachita bwino kwambiri pa ndewuyi. Kangapo kose yemwe ndimamenyana naye anagwa pansi. Koma ngakhale zili choncho, potengera kuti nkhonyayi inali mdziko la Tanzania, oyimbira anangompatsa mnyamata wa dziko lawoyo,” wadandaula Lano.

Pomwe ambiri amaganiza kuti Masamba ndi yemwe angapeleke mphatso ya nyuwele kwa a Malawi powina nkhonya yake, naye wapulumukira mkamwa mwa mbuzi kamba koti mzakeyo sanamusekelele koma kumuphidza nadzo dzibonyongo mpaka katswiri wa ku Malawi-u anayimika manja kupepesa.

Paja akulu akale anati mamuna nzako mpachulu, Masamba atasambitsidwa ndi zibakera mundime zinayi zoyambilira, anawona kuti angayambe kubwelera ku Malawi kuno ali ntembo, ndipo mundime ya chisanu, anangoimika manja kuli kuvomeleza kuti walephera ndipo oyimbira sanakachitira mwina koma kulengeza kuti Mtagi ndiye dolo.

Poti mvula ikagwa kuchuluka zoliralira, Masamba anadandaula kuti amamenyana ndi munthu yemwe thupi lake ndilolemera kwambiri kuposa iye zomwe akuti ndizosaloledwa pa malamulo.

“Ine ndimalemera ma kilogalamu (kg) 64 pamene amene ndimamenyana naye ndiwolemra ma Kg 69 kilogalamu. Ulendo wina ndizofumika kuti ochititsa masewero a nkhonya azionetsetsa kuti osewera asamasiyane kalemeledwe,” wadandaula Masamba.

Izi zikuchitika patangodutsa masiku ochepa pomweso nsalamangwe wina pa nkhonya mdziko muno Israel Kam’mwamba wathibulidwa ndi Aliya Phiri mu mpikisano wa African Boxing Union zomwe zapangitsa anthu ena mmasamba a nchezo kulangiza ochita masewerowa mdziko muno kuti azikamenya nkhonya zakunja akaona kuti azitolera nthanana.

Advertisement