Bambo wapha mkazi wake pomumenya m’mutu ndi mwala

Advertisement

Bambo wa zaka 32 yemwe dzina lake ndi  Dickson Kachikuni ali mu chitokosi cha a polisi ya pa Nkhunga ku Nkhotakota kamba kowaganizira kuti apha mkazi wawo Leah Ngoma wa zaka 21 pomumenya ndi mwala m’mutu  pomwe amagona usiku wapa 1 January.

Bamboyu akuti amaganizira kuti mkazi wakeyu anali ndi chibwenzi chamseli.

Mneneli wapolisi ya Nkhunga Sub inspector Andrew Kamanga wati  awiriwa anakwatirana chaka chatha koma aliyense amaganizira nzake kuti akuchita zibwezi zamseli ndipo izi zimadzetsa mikangano.

M’bandakucha wa pa 1 Januwale, a Kachikuni anafika kunyumba kwawo kuchoka komwa mowa ndipo anapeza akazi awo akugona. Iwo anakatenga chimwala ku bafa la panja ndipo anamenya nacho akazi awo m’mutu.

Kumenyedwaku kunapangitsa a Ngoma kuti afuule zomwe zinadzutsa anthu oyandikira nyumba omwe anakhamukira komweko ndipo anakapeza a Ngoma ali magazi okhaokha koma amuna awo atathawa.

Apolisi ndi a chipatala anapita kunyumbako komwe anapeza a Ngoma atamwalira chifukwa chotaya magazi ambiri.

Achitetezo a m’mudzi anayamba kusakasaka a Kachikuni ndipo anawapeza pamalo okwelera bus a Dwangwa pomwe amadikilira galimoto kuti athawe.

A Kachikuni akuyembekezereka kukaynkha mlandu wa mlanmdu okupha munthu.

Advertisement