Gulu la pa tsamba la mchezo lathandiza odwala pa chipatala cha Salima

Advertisement

Ngati njira imodzi yokondwelera nyengo ya khilisimisi komanso chaka chatsopano, gulu la pa tsamba la mchezo la WhatsApp la ‘Malawian  Gossip and Scandals’ linakachezela odwala pa chipatala chachikulu cha boma la Salima.

Gululi lapereka katundu osiyanasiyana wa ndalama pafupifupi K500  sauzande  kwa ana omwe agonekedwa pa chipatalachi ndipo akulandira thandizo la mankhwala.

Poyankhula atapereka thandizoli, wapampando wa gululi, a Ketrina Bazilio, ati adachitenga kukhala chinthu cha mtengo wapatali kuti apereke thandizoli komanso kupereka mawu a chilimbikitso kwa ana odwalawa komanso makolo awo.

Katundu yemwe gululi lapereka ndi monga sopo osambira komanso ochapira, sugar, mkaka, maheu, ndiwo za soya pieces, jiggies, kamba ndi zina zambiri.

M’mawu ake, mmodzi mwa ogwira ntchito pa chipatalachi a Yanjanani Mawindo adayamikira gulu la ‘Malawi Gossip and Scandals’ popereka thandizoli ponena kuti izi zithandizira pa umoyo wa odwala panthawi imene akulandira thandizo la mankhwala pa chipatalachi.

A Mawindo adalimbikitsa adindo komanso anthu ena akufuna kwabwino kuti atengerepo chitsanzo pa zomwe guluri lachita popititsa patsogolo ntchito zachifundo komanso umodzi.

Gulu la ‘Malawian Scandals and Gossip’ lidayamba mu chaka cha 2021 ngati malo anthabwala chabe koma kufika lero lagwira ntchito zachifundo zambiri mmadera osiyanasiyana mdziko muno.

Guluri lili ndi mamembala pafupifupi 70,200 ochokera m’maboma osiyanasiyana m’dziko lino.

Advertisement