Malipilo ku Israel: boma lati amene sakufuna asiye, apeleke mwayi kwa ena

Advertisement
a plane from Israel arrived in Lilongwe where it picked up over 200 young Malawians who have since arrived in Israel today.

Pomwe pali kusamvana pa nkhani yamalipiro pakati pa achinyamata omwe akugwira ntchito mdziko la Israel ndi ma agent omwe adawatumiza mdzikolo, boma kudzera mwa Kazembe woimila Malawi ku Israel lati achinyamata omwe sakufuna kuti ndalama zawo zidzilowa ku banki, anene ndipo ndege yowabweletsa kuno kumpanje ilipo kale.

Nkhaniyi yayamba pomwe achinyamata ena omwe ali mdziko la Israel anauza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno kuti iwo ndiwokwiya kamba koti ma ajenti (agent) akuwakakamiza kuti asayinire zikalata zomwe zikusonyeza kuti malipiro awo a pamwezi adzipita ku maakaunti a ma ajenti-wo.

Achinyamatawa ati zikalata zomwe akukakamizidwa kuti asayinilezo zikusonyeza kuti malipirowo akafika ku akaunti ya ma ajentiwo, iwowo (ma ajenti) adziwatumiza ku ma akaunti a achinyamatawa omwe anatsekula kuno ku Malawi pa nthawi yomwe amakozekera ulendo wawo opita mdzikolo (Israel).

Achinyamatawa ati izi sakugwirizana nazo ponena kuti ntchito akugwira ndi iwowo osati ma ajentiwo, ndiye anayenera kuwapatsa ndalamazo kuti iwowo pawokha azizitumiza ku Malawi kumo kudzera ku ma akaunti awo kapena ma akaunti a mabwana awo ndipo ati akuona ngati atha kudyeledwa masuku pa mutu.

Koma poyankhapo kudzera mu kalata yomwe yatulutsidwa Lachinayi pa 28 December, 2023, boma la Malawi kudzera mwa kazembe wake wa ulemu mdziko la Israel, lati zomwe zikuchitikazi palibe cholakwika chili chose kamba koti ndi zomwe zili mu mgwirizano omwe achinyamatawa anasayinira asanapite mdziko la Israel.

“Monga kazembe waulemu wa dziko la Malawi ku Israel, komanso ngati wopereka ndalama pa mwayi kwa atsikana ndi anyamata kupeza chilolezo chogwira ntchito ku Israel, zomwe sizingapindulitse ogwira ntchitowo ndi mabanja okha komanso dziko lomwe likufunika kwambiri ndalama zakunja kuti limange tsogolo labwino kwa nzika zonse za Malawi, ndikuyenera kukukumbutsani nonse kuti ndi gawo la mgwirizano wanu wa ntchito komaso chilolezo chogwilira ntchito yanu (Visa) kuti malipiro onse azilipidwa mu USD kuma akaunti anu omwe munatsegula ku Malawi,” yatelo kalatayi.

Ofesi ya kazembe waulemuyi yanenetsa kuti zomwe achinyamatawa akufuna sizichitika ndipo yapeleka mwayi oti wachinyamata yemwe akuona kuti sakwanitsa, anene ndicholinga choti amubweletse kuno kuti apelekeso mwayi kwa achinyamata ena omwe adzakwanitse kutsata malamulo amgwirizanowu.

“Palibe malipiro omwe adzalipidwe ku Israeli kapena kuperekedwa pamanja kwa wina aliyense, ndalama mungathe kupatsidwa pamanja ndi okulembani ntchito ndi zosapitirira 10% ya malipiro anu.

“Kulankhulana uku ndikofunikira kwa onse ogwira ntchito m’mafamu, mafakitale, ndi mahotela. Ngati wina sali wokonzeka kuchita mogwirizana ndi mgwirizanowu, ali ndi ufulu kulumikizana ndi kampani imene inawapezera mwayi (Recruitment Agency) ndikupempha kuti abwerere ku mudzi ndikupeleka visa yake kwa aliyense amene ali wokonzeka kulemekeza ntchito,” yateloso mbali ina ya kalatayi.

Boma la Israel linachita mgwirizano ndi boma la Malawi ndipo mugwirizanowu, a Malawi osachepera 5000 akuyembekezeka kupita kukagwira ntchito zosiyanasiyana ku Israel.

Advertisement