Anthu atatu amangidwa kamba kokupha munthu yemwe anagwidwa akuba nkhuku

Advertisement

Apolisi ku Kasungu atsekera mchitokosi anthu atatu omwe akuwaganizira kuti anapha bambo wa zaka 38 yemwe adamugwira akuba nkhuku.

Anthuwa, ndi a Simon Genesis a zaka 40, Kachule Gwilire, a zaka 53 Komanso a Chrisy Genesis a zaka 53, onsewa a m’mudzi mwa a Genesis mfumu yaikulu Kasichi m’bomali.

Malingana ndi a Joseph Kachikho omwe ndi wofalitsa nkhani za polisi m’bomali, anthuwa akuwaganizira kuti anapha a Peter Phiri.

A Kachikho ati a Phiri adasowa kumayambiriro kwa November ndipo abale awo anakanena ku polisi ya Ndonda za kusowaku.

A polisi adayamba kafukufuku yemwe anaonetsa kuti atatuwa amadziwapo kanthu za imfayi.

Zinadziwika kuti a Phiri adagwidwa akuba nkhuku ndipo anthuwa adawapha a Phiri ndikukwilirira thupi lawo m’dzenje.

Apolisi ndi achipatala anakafukula thupilo ndipo atalipima, achipatala apeza kuti a Phiri adamwalira kaamba kovulala m’mutu.

Anthuwa ali mchitokosi cha apolisi ndipo akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu.

Advertisement