Chamba chathilidwa moto ndi apolisi

Advertisement
Malawi Police have burnt Chamba in Dowa

Matani a chamba olemera makilogalamu oposa 1,150 omwe analandidwa kwa anthu osiyanasiyana chaka chino athilidwa moto ndi apolisi ku Mponela m’boma la Dowa dzulo.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Macpstson Msadala, apolisi atentha chambachi chomwe njonda zina zinkafuna kuzembetsa kanunduyu.

Kutenthedwa kwa katunduyu ndi malingana ndi ndondomeko zomwe adakhazikitsa kuti chambachi achithire moto akamaliza kuzenga milanduyi pasanathe masiku asanu ndi awili.

Pamwambo otentha chambachi panali anthu osiyanasiyana omwe anabwera kudzachitira umboni monga a First Grade Magistrate Talakwanji M’ndala, Superintendent Lonnie Mjale, a mabungwe osiyanasiyana, Namalamba wa pa polisi ya Dowa, komanso atolankhani.

Chambachi ndi chomwe apolisi m’bomali akhala akulanda pa malo osiyanasiyana ochitira chipikisheni maka munsewu wa M-1.

M’masiku apitawo apolisi maboma monga Salima adatenthanso chambachi atamaliza kuzenga milandu yokhudza za mankhwala ozunguza bongowa.

Advertisement