Mabodza: Nkhani ya nyama ya galu siyinachitike ku Malawi

Advertisement
Malawi Nyama ya Galu

Malawi24 yapeza kuti nkhani yomwe ikuyenda m’masamba a mchezo yoti anthu amagulitsa nyama ya galu ku Dowa siyinachitike ku Malawi.

Pa masamba a mchezo a pa Fesibuku kuyambila dzulo madzulo pabuka nkhani yokuti anthu atatu amangidwa ku Dowa chifukwa anawapeza akugulitsa nyama ya galu yophikaphika pa chiwaya. Ena atengera nkhani yomweyi ku X komwe akuti izi zinachitika ku 23 ku Lilongwe.

Zithunzi zomwe zawanda mu masamba a mchezo zikuonetsa amayi amodzi ndi abambo awiri akuoneka kuti agwidwa. Zithunzi zina zikuonetsa  nyama ya galu ili mu beseni, mutu wa galu komanso nyama ina yokazingidwa ili pa chiwaya limodzi ndi tchipisi.

“Zachitika kumasanaku (21 Disembala) akuti mzimayi mukumuona apapayu  wagwidwa pamodzi ndi anyamata ake antchito pomwe apezeka akudyetsa anthu Chips  ndi nyama ya Galu,” uthenga omwe ukugawidwawo ukumatero.

Koma Malawi24 itafufuza mbiri ya zinthunzizi pa intaneti, yapeza kuti zithunzizi zinaikidwa koyamba pa tsamba la fesibuku lomwe amaikapo zochitika ku Angola. Tsambali linaika izi pa 14 Disembala chaka chino, sabata limodzi nkhaniyi isanayambe kubuka kuno ku Malawi.

Malingana ndi tsamba la pa Fesibuku la Alo Lucapa, anthu atatuwa anamangidwa ku Lunda-Norte mu mzinda wa Dundo ku Angola atawapeza atapha nyama ya galu.

“Anthuwa amauza ma kasitomala kuti nyamayi ndi ya mbuzi ndipo ma kasitomala amakhulupirira,” latero tsambali.

Potsimikiza zomwe yapeza Malawi24, woyankhulila apolisi ku Dowa a Alice Sitima atinso apolisi sakudziwapo kanthu pa nkhani yotereyi ndipo nawo angodabwa ndi zomwe zikuyenda mu masamba a mchezo.

Advertisement