A Msonda amafuna kulanda katundu ku DHL

Advertisement
DPP poltician Ken Msonda

M’modzi wa akuluakulu a chipani cha DPP a Ken Msonda lero amafuna kukalanda katundu ku ofesi ya DHL ku Lilongwe ponena kuti kampaniyo inakanika kutumiza lita limodzi la mankhwala azitsamba obwezeretsera chitetezo mthupi omwe a Msonda amatumiza ku Botswana.

Malingana ndi zomwe yalemba Zodiak, a Msonda pa 28 November chaka chino adapita ku ofesi ya DHL kukatumiza mankhwalawa kwa mwana wawo wokhala  ku Botswana. Iwo adalipira ndalama yokwana K100,000 ndipo adauzidwa kuti mankhwalawo afika ku Botswana mu masiku atatu.

Pa 11 December a Msonda adalembera kampaniyi kudandaula kuti mankhwalawa sanafike koma DHL akuti simakambabe zomveka.

Pokwiya ndi kuchedwaku, a Msonda lero anapita ku DHL ku Lilongwe ndi anthu olanda katundu. Kanema yemwe ajambula a Zodiak akuonetsa m’modzi mwa ziphona zolanda katunduzo akuyesa kuchotsa TV pakhoma ku ofesiyi.

Koma mu mawu awo mu kanemayi, akuluakulu a kampani ya DHL anati mankhwalawa anatumizidwa ku Botswana mu nthawi yake koma olandilayo akuyenera kupereka 421 Pula (K54,000) ngati msonkho ndipo izi a ku DHL sizili m’manja mwawo

A DHL anaonetsa kukhumudwa ndi zomwe achita a Msonda zofuna kukalanda katundu ku ofesi ya DHL.

Komabe malingana ndi Zodiak, a DHL ati  awabwezera a Msonda ndalama zawo posafuna kulimbana nawo.

Advertisement