A zanyengo apempha a Malawi kuti akhale osamala pamene mvula ya mphamvu ikhale ikugwa

Advertisement
Heavy rains are expected to hit Malaiw

Nthambi yoona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo m’dziko lino lachenjeza a Malawi maka akuchigawo chakum’mwera ponena kuti lero pa 14 December 2023, mvula yamphamvu ikhale ikugwa.

Malingana ndi uthenga omwe watulutsa ndi  mneneli wa nthambiyi, a Yobu Kachiwanda ati mvula ya mphepo ndi yamkuntho ikuyembekezereka kugwa maka mchigawo chakum’mwera ndipo ati kotero nkofunika kuti anthu akhale osamala maka pamene mvulayi ikugwa.

Mvula yamphamvu ikupitilirabe kugwa m’madera osiyanasiyana mdziko muno kotero a Malawi akuyenera kukhala m’malo otetezeka pamene mvula ikugwa.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement