Mphunzitsi amupeza osalakwa pa mlandu ogwililira mwana


Bwalo la milandu mu mzinda wa Zomba lapeza Chisomo Francisco Gomani, yemwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya pulaimale, wosalakwa pa mlandu womuganizila kuti anagwililira  mwana wachichepere.

Gomani adamangidwa ndi polisi ya Chingale pa 27 October 2023 pomuganizila kuti adagonana ndi mwana yemwe anali wophunzira pa sukulu yomwe iyeyu amaphunzitsapo.

Atamangidwa, wachibale wake Temweka Chirwa, anapita kukapempha thandizo ku ofesi ya Legal Aid Bureau ndipo mlanduwu adautenga loya Hanleck Ching’anda mothandizidwa ndi Tadala Ching’amba.

Kubwalo la milandu, woganizilidwayu adaukana mlanduwu ndipo udapitilira ndithu. Mbali ya boma idati ibwera ndi mboni zawo zitatu zomwe zinali mayi a mwanayu, mwanayu komanso kadaulo wa zachipatala.

Umboni womwe mayi amwanayu anapereka kubwalo la milandu unali wakuti pa 27 October 2023, mkazi wa Gomani, yemwe ndi mchemwali wa mayiyu, anagogoda kunyumba kwake usiku ndikumuuza kuti wapeza mwana wawo ali mnyumba ina ndi Gomani. Mayi amwanayu atapita kunyumbayo akuti adamupezadi Gomani ndi mwanayo, koma mwanayo adathawa.

Adaonjezeranso kuti pamodzi ndi mchemwali wawo, pamalopo adapezapo kondomu yomwe akuti idali ndi magazi.

Mboni yachiwiri, Catherine Maganizo yemwe amagwira ntchito ku chipatala, adauza bwaloli kuti adamupima mwanayo ndikupeza kuti adagonanapo ndi mamuna kangapo konse.

Mwanayu kumbali yake adauza bwaloli kuti patsikulo adapita kunyumba kwa woganizilidwayo limodzi ndi nzake kuti akathandize kuchonga mayeso, koma sadanenepo kalikonse kokhudza kugonana ndi Gomani. Kwa masiku awiri akuperekela umboni, mwanayu sanatchulepo kalikonse kokhudza nkhani yomwe apolisi anammangila mphunzitsiyu.

Umboni wa boma utaperekedwa, Legal Aid Bureau idatsindika kuti woganizilidwayu alibe mlandu wakuti ayankhe chifukwa umboni womwe bwalo linapatsidwa sudali wogwira mtima.

Loya Ching’anda adapitirizanso kunena kuti mayi amwanayu anabwera ndi umboni womwe unali mphekesela, kondomu yomwe adatchula sanabwere nayo komanso mwanayo sadauze bwalo kuti nkhaniyo ndiyoona.

Mchigamulo chake, woweruza milandu a Martin Chipofya adagwirizana ndi Legal Aid Bureau kuti ambali ya boma sanabwere ndi umboni wokwanila wotsimikiza kuti Gomani anagonana ndi mwana wachichepere. Bwaloli lidaonanso kuti umboni unali wosakwana ndinso wosadalilika kuti mpaka munthu amangidwe.

Bwalo kotero lidapeza mphunzitsiyu kuti alibe mlandu woti ayankhe malingana ndi zomwe amaganizilidwa. Gomani tsopano ndi mfulu.

Alemba ndi a Legal Aid Bureau