A Kalindo akhalabe mkambolimboli uku akudikira chigamulo

Advertisement
Malawi Protests leader Bon Kalindo has been arrested on several occassions since he started leading demonstrations against the Lazarus Chakwera administration

A Bon Kalindo akhala akusungidwabe mchitokosi cha apolisi uku akudikira chigamulo kuchokera kwa woweruza milandu a Muhammad Maxwell Chande lachisanu likudzali pa 15 December.

A Kalindo anawanjata sabata latha m’boma la Zomba powaganizira kuti iwo anayambitsa chisokonezo komanso ziwawa pa zionetsero zomwe zidachitika kumapeto a mwezi watha m’boma la Zomba.

A Kalindo akhala akutsogolera zionetsero monga m’maboma a Zomba, Blantyre, Mangochi, komanso Mzuzu.

Mwazina iwo akhala akutsogolera zionetserozi kamba  kamavuto omwe akuta dziko lino monga kugwa kwa mphamvu kwa kwacha, kulephera kwa boma kulemba ntchito achinyamata komanso zokhudza zipangizo za ulimi zotsika mtengo.

Ku zionetsero za ku Zomba ndi Mangochi, anthu anaphwanya galimoto komanso kuba katundu mu masitolo. Apolisi anachita kuphulitsa utsi oketsa misozi kuti anthuwa athawe.

Sabata latha, a Kalindo anaonekera ku bwalo la milandu ku Zomba pa mulandu okhudza ziwawa za ku Zomba koma atawapatsa belo apolisi anawanjatanso ndikuwapitittsa ku Mangochi kuti akayankhenso mulandu ngati omwewu.

Advertisement