‘Zigawenga’ zamulavula Salanje


Hastings Salanje Malawian Pastor

Akuluakulu a mpingo wa God’s Chapel alengeza kuti zigawenga zomwe zinasowetsa mtsogoleri wawo Hastings Salanje masiku angapo apitawa, zamulavura tsopano ndipo ali bwino bwino.

Pa 1 December chaka chino, akuluakulu a mpingo wa God’s Chapel anabwera poyera ndikulengeza kuti a Salanje abedwa ndi zigawenga zina pomwe iwo pamodzi ndi akuluakulu ena anali ndi zokambirana pa kachisi chawo m’dziko la South Africa.

Patadutsa masiku khumi (10), m’busayu atasowetsedwa ndi zigandangazi, akuluakulu a mpingowu alengezaso kuti a Salanje atulutsidwa ku malo komwe amasungidwako.

Malingana ndi zomwe zalembedwa pa tsamba la fesibuku la a Salanje, anthu achipongwewa awatulutsa abusawa usiku wa la Mulungu pa 10 December, 2023 ndipo akuti anakawasiya pa malo otchedwa Katlehong m’dziko lomwelo.

“Shalom kwa akhristu onse a God’s Chapel Ministries komanso otsatira a Pastor Hastings Salanje. Ndife okondwa kulengeza kuti Atate Wathu muuzimu; Pr Hastings Salanje watulutsidwa ndi omwe adamuba usiku watha ndipo adatsitsidwa pafupi ndi malo ogulitsira zinthu ku Katlehong, JHB, RSA,” watelo uthenga omwe walembedwa mchizungu pa tsamba la fesibuku la Salanje.

Kupatula apo, m’modzi mwa abusa a mpingowu a Nelson Mlotha, awuza imodzi mwa nyumba zofalitsa nkhani m’dziko muno kuti m’busa Salanje wapezeka pomwe akuluakulu ampingowu apereka ndalama kwa achiwembuwa kuti awamasule.

Mpingowu wathokoza aliyense amene anayima nawo m’mapemphero ndi chithandizo panthawiyi ndipo akuti a Salanje ayankhula kudzera mu kanema yemwe agawidwe malo osiyanasiyana madzulo a lero lolemba.