Mvula ya mphepo yawononga sukulu ku Dedza

Advertisement
School Blocks

Mvula yomwe inadza ya Mphamvu ndi mphepo yawononga sukulu ya pulayimale ya Mkhaza ku Linthipe 1 m’boma la Dedza.

Malingana ndi m’modzi mwa aphunzitsi yemwe walankhula ndi Malawi24 a Josen Chaima ati Mvulayi inayamba dzulo lachitatu Masana koma inabwera ndi mphepo yamphamvu zomwe zinapangitsa kalasi limodzi kusasuka Malata.

A Chaima ati ngoziyi sinavulaze aliyense pa nthawi yomwe imachitika chifukwa mwa mwayi ana mkalasili anali ataweluka kale.

Izi zikudza pamene a bungwe lowona za nyengo snalengeza kuti kuyambila pa 04 mpaka pa 10 December ma dela ena mdziko muno alandila mvula yamphamvu yodza ndi Mabingu ndi mphepo kamba ka kusakhazikika kwa Mphepo yofunda ndi yosakhazikika yochokera kumvuma.

A zanyengo alangiza anthu mu chikalata chawo kuti kawirikawiri Mvula ya mabingu imadza ndi mphenzi komanso mphepo ya mkuntho kotero anthu azibisala malo otetezeka bwino mvulayi ikamagwa , anthu awonetsetse kuti nyumba zawo zili zolimba ku mphepo za mkuntho.

Advertisement