Lonjezo linadulitsa mutu wa Yohane: Osewera a Scorchers sanapatsidwebe ndalama zolonjezedwa

Advertisement
Malawi National Netball Team Celebrates winning the Cosafa Women's Championship following victory over Zambia in South Africa on 15 October, 2023

Asungwana okankha chikopa mu timu ya dziko lino ya Scorchers, akuyimba nyimbo ya Joseph Nkasa ya ‘Anamva’ pomwe akuti bungwe loyendetsa mpira la FAM silinawapatsebe ndalama zomwe linalonjeza kuphatikiza K10 miliyoni yomwe mneneri Shepherd Bushiri anafupa atsikanawa kuti agawane.

Izi ndi malingana ndi zomwe tsamba lino lapeza pa masamba anchezo kuphatikizapo pa tsamba lotchuka lolemba nkhani za masewolo la ‘Wa Ganyu’ lomwe lati linayankhula ndi m’modzi mwa osewerawa yemwe waulura zambiri za nkhaniyi.

Malingana ndi tsamba la fesibuku la Wa Ganyu, atsikanawa omwe anadoda chikopa mochititsa kaso kwambiri ndipo anatenga chikho cha COSAFA mwezi wa October chaka chino, akuyang’ananirabe ku njira kuti mwina bungwe loyendetsa masewero la Football Association of Malawi liwaponyera kanganyase kawo komwe  likuwasungira.

Bungwe la FAM likuyenera kupeleka 1 miliyoni kwacha kwa mtsikana aliyese, 1 miliyoni kwacha ina yomwe FAM inalonjeza ngati mphoto ya padera komaso K500,000 ngati ma alawasi (allowance) kwa mtsikana aliyese amene anasewerako pa masewero onse omwe timuyi inali nawo ku mpikisano omwe unachitikira m’dzikola South Africa.

Kuphatikiza zonse pamodzi, osewera m’modzi akuyembekezeka kulandira ndalama yosachepera 2.5 miliyoni kwacha kuchokera ku bungwe la FAM komaso kupatula apo, atsikanawa anapatsidwa 10 miliyoni kwacha kuchokera kwa mneneri Bushiri kuti agawane yomwe akuti mpaka pano sanalandilebe ngakhale 1 tambala.

Osewerayu yemwe akuti sanafune kutchulidwa dzina, wauza tsamba la Wa Ganyu kuti atsikanawa ayesetsa kufikira atsogoleri a osewerawa kuti awalondolezere za ndalama zawozi koma akuti palibe chomwe chikuchitika kufikira pano pomwe padutsa miyezi iwiri tsopano.

“Osewera aliyense akuyenera kupatsidwa ndalama zosachepera 2.5 miliyoni kwacha. Tinapempha ma captain athu kuti atsate nkhaniyi koma palibe chomwe chikuchitika. Nawoso a Team manager tidawafikira koma palibe chomwe chikuchitika. Tinafikiraso mtsogoleri wa mpira wa miyendo wa amayi yemwe adatitumiza ku HOD (Head Of Delegation) komwe sitinalandire thandizo lililonse. Kenako tidafunsa akuluakulu a FAM koma nawoso sanayankhe,” wadandaula osewera wina wa Scorchers.

Potsatira nkhaniyi, anthu ambiri makamaka patsamba la nchezo la fesibuku ati izi ndizodandaulitsa kwambiri komaso ena ati izi zili ndikuthekera koti atsikanawa asalimbikireso ulendo wina zomwe akuti zingapangitse kuti masewero a mpira wa miyendo wa amayi alowe pansi m’dziko muno.

Pakadali pano akuluakulu a bungwe la FAM sanaikilepo ndemanga za nkhaniyi komaso sanabwere poyera ndikufotokoza zifukwa zimene bungweli lachedwera kupeleka ndalama ma alawasi komaso zomwe linalonjeza kwa osewera aliyese yemwe anatenga nawo gawo ku mpikisanowu.

Timu ya Scorchers inatenga chikho cha COSAFA pamutu pa timu ya Zambia yomwe inathambitsidwa ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi mu “finals” ndipo Scorchers inapambana masewero asanu onse omwe inali nawo ku mpikisanowu.

Advertisement