Kulibe kothawira, mowa wakwera mtengo


Anthu okondana chakumwa choyankhulitsa chizungu chija akuyenera kuyamba kulingalira zosiya kumwa chakumwachi ndikuyamba kumwa fanta osaboola mthumba kamba koti kampani yofulula mowa ya Castel yakweza mitengo ya mowa omwe imapanga kuphatikizapo ‘baby gin’.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe kampani ya Castel Malawi Limited yatulutsa lachinayi pa 30 December, 2023 chomwe chikusonyeza mitengo ya tsopano ya zakumwa zaukali zomwe imapanga.

Chikalatachi chomwe chasayinidwa ndi m’modzi wa akuluakulu a kampaniyi a Johan Maree cgati mitengo ya tsopanoyi iyamba kugwira ntchito lachisanu pa 1 December, 2023

Kampaniyi yati kuyambira pa 1 December, 2023 botolo la 330ml la mowa wa Castel lachoka pa mtengo wa K900 kufika pa mtengo wa K1000 tsopano ndipo mabotolo a 330ml a Carlsberg Green komanso Special, afika pa mtengo wa K1,300.

Mbali inayi, botolo laling’ono la Malawi Gin lomwe kampaniyi inabweretsa kumayambiliro a chaka chino komaso botolo la 330ml la Vodka, tsopano lafika pa K3500 kuchoka pa K2500 pomwe mbali inayi botolo la 750ml la Premier Brandy lili pa K14,000.

Izi zikudza kutsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya kwacha ndi 44 “percent” kumayambiliro kwa mwezi wa November chaka chino.