Zipolowe zidabuka ku Zomba apolisi ataphulitsa utsi okhetsa misozi

Advertisement

Chipwirikiti chidabuka dzulo madzulo kwa Chikanda, Kazembe, Mpondabwino mu mzinda wa Zomba apolisi ataphulitsa utsi okhetsa misozi pambuyo padziwonesero zomwe adatsogolera ndi mkulu wa gulu la Malawi First a Bon Kalindo.

Zipolowezi zidayamba pomwe anthu ozungulira mdera la Mpondabwino adakathyola nyumba yawa polisi wina ndikubamo katundu komanso kuba mizimbe nkatikati mwa police college.

Zipolowezi zidapitilira mpaka 8 koloko usiku ndipo zidakafika pafupi ndiku University ya Malawi (Chanco) zomwe zidasokonedza achinyamata omwe amaphunzira ku sukulu ya ukachenjedeyi.

Pazipolowezi, anthu okwiya amdera la Chikanda adakabanso malata ndi zinthu zina zomwe akumangira nyumba za apolisi chifukwa chokwiya ndi utsi okhetsa misoziyo.

Ntchito za malonda kwa Mpondabwino ndimadera ena zidatsokekera chifukwa anthu adathawa kusiya nyumba zawo kukabisala ndipo ena adathawa mpaka kukafika kwa Mpunga, Sadzi Thundu ndipo anthu ambiri adathamangira nawo kuchipatala chachikulu cha Zomba chifukwa chokomoka komanso kubanika chifukwa cholephera kupuma.

Padakali pano, chiwerengero cha anthu ovulala komanso cha anthu omwe amangidwa sichikudziwika.

Poyankhula ndi Malawi24, wofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chaku mmawa Superintendent Patrick Mussa wati pakali pano apolisi akufufuza kuti agwile anthu omwe adakukhudzidwa ndi kuba katundu nyumba komanso kuwononga nyumba zomwe zikumangidwa za apolisi.

Superintendent Mussa wati apolisi adaphulitsa utsi wokhetsa misozi pofuna kubalalitsa anthu omwe adali ndimaganizo ochita zawupandu.

Advertisement