Ulamuliro wa a Chakwera waonetsa chidwi chothana ndi katangale, atero a Chizuma


Malawi Corruption Lazarus Chakwera

A Martha Chizuma omwe ndi mkulu wabungwe lothana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) ati utsogoleri wa a Lazarus Chakwera waonetsa chidwi chothana ndi katangale m’dziko la Malawi.

Mkulu wabungweli amayankhula izi ku nkumano omwe umachitika dzulo mu mzinda wa Lilongwe ku BICC okhudza zakatangale.

Iwo anati pa zaka 25 zomwe bungweli lakhala likutumikira m’dziko lino, lakhala likukumana ndi mavuto ankhaninkhani monga kusowekera chidwi kuchokera kwa atsogoleri komanso kusowekera kwa ndalama zogwirira ntchito

Koma a Chizuma anati boma la a Chakwera likuchita chothekera kuti bungweli lizigwira ntchito yake yothana ndi katangale.

Iwo anaonjezera kunena kuti pakadali pano bungweli likugwira ntchito zake moyenera kamba kakuti palibe kuopsezedwa kulikonse kuchokera kwa omwe ali andale.

A Chizuma anaonjezera kunena kuti boma la a Chakwera linalola kuti a Malawi azibwera pamodzi ndikukambilana nkhani za m’mene dziko lino lingathanilane ndi mchitidwe wa katangale.

Mawu a Chizuma akudza patatha pafupifupi chaka kuchoka nthawi yomwe a Chizuma anawamanga ku nyumba kwawo mu Disembala chaka chatha pa mlandu woti ananena akuluakulu ena a m’boma ndi ochita malonda kuti amachita zakatangale.

Wolemba: Ben Bongololo