Ndege yomwe ikuyembekezeka kunyamula a Malawi oposa 200 omwe boma likuti lawapezera ntchito m’dziko la Israel, yafika kale m’dziko muno ndipo anthuwa anyamuka pakati pausiku lero.
Ndege yonyamula anthuwa yomwe ndiya aRKIA Airbus a321-251NX, inatela pa bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe momwe nthawi imati 1:42 lero lachisanu pa 24 November, 2023 ndipo akuluakulu ena atsina khutu nyumba ina yofalitsira nkhani kuti ndegeyi ibwelera ku Israel pakati pausiku lero.
Malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti ndegeyi inyamuka kubwelera ku Israel ndi anthu 221 omwe akuyembekezeka kukagwira ntchito za kumunda m’dziko la Israel ndipo zikusonyeza kuti boma la Malawi ndilomwe lawapezera anthuwa ntchitoyi.
Izi zikudza pomwe mtsogoleri wa mbali yotsutsa mu nyumba ya Malamulo, a Kondwani Nankhumwa, lachiwiri anabenthura kuti m’dziko muno mukuyembekezeka kufika ndege kuchokera m’dziko la Israel kudzatenga achinyamata 221 kuti akagwire ntchito zakumunda mu dziko la Israel.
Patsikuli Nankhumwa anapempha unduna wa za ntchito kuti ufotokoze chilungamo chenicheni pa za ntchito yomwe achinyamata akukagwira mu dziko la Israel ponena kuti panaliso mphekesera kuti achinyamatawa akukamenya nkhondo ya dziko la Israel ndi dziko la Palestine.
Izi zinabweretsa mapokoso m’nyumba ya malamuloyi kamba koti akuluakulu ambali ya boma anapempha a Nankhumwa kuti abweze zomwe ayankhulazi ndikubweretsa umboni weniweni wa nkhaniyi.