Kalindo akuchititsa zionetsero ku Zomba

Advertisement

Mtsogoleri wa Malawi First Bon Kalindo ali mu mzinda wa Zomba kuchita ziwonetsero zosakondwa ndi kugwa kwa mphamvu ya kwacha, kukwera kwa mitengo ya zinthu komanso kuchepa kwa malipiro anthu ogwira ntchito Boma.

Ziwonetserozi zayambira pa bwalo laza masewero la Zomba Community Ground mpaka akapereke chikalata chamadandaulo ku office ya Bwana Mkubwa wa Boma la Zomba ndipo kwafika anthu ochuluka komanso kwafika apolisi ochuluka kupereka chitetedzo

Poyankhula ndi Malawi24, Bon Kalindo wati anthu dziko muno akuvutika kwambiri chifukwa zinthu zofunika pamoyo wamunthu zakwera mtengo ngakhale mafuta agalimoto.

Kalindo wadzudzula mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera chifukwa chosamva madandaulo a Malawi komanso chifukwa chovomereza kuti ndalama ya kwacha ichepe mphamvu.

“Zinthu ku Malawi kuno sidzikuyenda ndipo anthu ambiri akugona ndi njala chifukwa chosowa chokudya komanso zinthu zakwela mtengo chifukwa chokutsika mphamvu kwa ndalama ya kwacha.” Adatero Kalindo.

Iye wayamikira anthu amu mzinda wa Zomba chifukwa chobwera mwa unyinji kudzakhala nawo padziwonetserodzo.

Dzulo, a Kalindo dzulo anachititsanso zionetsero mu mzinda wa Blantyre komwe iwo anakwanitsa kukapereka chikalata kwa bwanamkubwa wa mzindawu.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement