Mipando ya ‘blue’ kuno ayi – phungu wati mtundu wa mipando ku nyumba ya malamulo usinthidwe

Advertisement
Parliament of Malawo

Phungu wa chipani cha Malawi Congress Party m’dera lakumwera kwa boma la Dedza a Ishmael Onani, wabwereza kupeleka pempho lomwe a kuti anamutuma ndi anthu akudera lake loti mtundu wa mipando m’nyumba ya malamulo usinthidwe usakhaleso ‘blue’.

A Onani amayankhula izi lachisanu pa 17 November pomwe aphungu anyumba ya malamulo akupitilira kuwunikira ndondomeko ya zachuma ya pakati pa chaka ya 2023/2024.

Phunguyu wati amakumbutsa za ndondomeko yosintha mipandoyi yomwe a kuti anthu akudera lake anamutuma kuti akapemphe m’mbuyomu ndipo wanenetsa za kufunika kosintha mtundu wa mipando m’nyumba ya malamuloyi.

Iwo ati angakhale okondwa ngati mtundu wa ‘blue’ omwe mipandoyi inakutilidwa ungasinthidwe ndi mtundu uli onse omwe uli pa mbendera ya dziko lino yomwe ndi mitundu yobiliwira, yofiira komaso wakuda (green, black and red).

“Anthu aku Dedza South anayima chaka ndi theka ngati si zaka ziwiri zapitalo pankhani ya mitundu ya mipando yathu. Mitundu siikugwirizana ndi mitundu yomwe ilipo pa mbendera ya dziko lathu ndipo munatilonjeza kuti tiwona kusintha, izi zichotsedwa ‘madam speaker’.

“Anthu a ku Dedza ndiodandaula kwambiri kuti mpaka pano, tikutha kuona mipando ya ‘blue’ pamene bwezi tikuona mipando yakuda, yofiira kapena yobiriwira. Mutiuze kuti vuto ndi chiyani ‘madam speaker’?” wafusa Onani.

Ndipo poyankha za fusoli sipikila wanyumbayi a Catherine Gotani Hara ati adzayankha zankhaniyi mtsogolomu.

“Ndamva funso lanu, yankho lidzabwera panthawi yoyenera,” anayankha choncho Gotani Hara.

Advertisement