A Malawi mumva kuwawa – Chakwera

Advertisement
Malawian President, Lazarus Chakwera

Pulezidenti wa dziko lino Lazarus Chakwera wati aMalawi amva kuwawa kwa miyezi ikubwerayi potsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha.

A Chakwera ananena izi usiku wa lachitatu pomwe amayankhula kwa mtundu wa aMalawi kuchokera ku nyuma ya ufuma ya Kamuzu.

A Chakwera anakumbutsa aMalawi kuti m’mene ankalumbiritsidwa mu chaka cha 2020 ananena kale kuti kukonzaso chuma dziko lino kukhala ngati fupa lathyoka ndipo kuti likonzeke pafunika kuti ululu ukhalepo.

“Ndiye ndizomwe tikumva pano. Tikumva kuwawa pakali pano ndipo timva kuwawa kwa miyezi yochepa ili kutsogoloku kufikila mafupa onse atakhala bwino ndipo kenako tizakondwera mu nthawi yakututa chifukwa ili pafupi.

“Nthawi yakututayi ibwera pokhapokha ifeyo tigwiritse ntchito zachitika panozi moyenera,” anatero a Chakwera.

Iwo anati kuchepetsedwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha kwapweteka aliyense ndipo ndikofunika kuti aliyense agwiritse bwino ntchito ndalama, osati kungomwaza.

Apa iwo anati asiya kuyenda maulendo akunja kuyambira lero ncholinga chowonetsetsa kuti ndalama za dziko lino zikugwira ntchito moyenera.

Iwo anati  nduna zonse za boma zimene zinapita komanso zidakali mayiko akunja pa ndalama za aMalawi zikuyenera kubwerera pambuyo nkudzakhala kuno ku kumudzi kuti chuma cha dziko lino chitetedzedwe.

 A Chakwera anatinso nduna zonse kuyambira lero zikuyenera kuyamba kulandira theka la mafuta omwe zimalandira.

“Ndauza  a nduna azachuma kuti mu bajeti ikubwerayi ayikemonso thandizo la anthu opanga mabizinesi ang’onoang’ono kuti apeze popumira komanso ndawauza andunawo kuti bajeti imeneyi awonetsetsenso kuti pali ka gawo koyenera kuti onse ogwira ntchito m’boma nawonso athandizike apezeko mpumiro.

“Ndawauzanso padakali pano ayambenso kuona za misonkho yomwe anthu amapereka kuti atha kuganizira kuti mlingo wanji akuyenera kukhalapo,” atero a Chakwera.

Iwo achenjeza ochita malonda kuti asiye khalidwe lokweza malonda awo mulimonse ndipo ati powonetsetsa kuti izi zitheke ati a nduna a za chuma komanso oyang’anira malonda  agwire ntchito pamodzi ndi  owona za malonda kufufuza wina aliyense komanso kuwona mitengo kuti ilibwanji.

Pomaliza ati ndalama zonse zomwe angapeze panjira zimenezi zizagwila ntchito yogulila feteleza komanso chakudya kuti pamene anthu akupita kodzala kuminda akhale kuti ali ndi chakudya pakhomo pawo.

Advertisement