Nduna ya zachuma yathawa mafunso

Advertisement
Malawi Finance Minister

Nduna ya Zachuma a Simplex Chithyola Banda m’mawa uno yasiya atolakhani kukamwa kuli pululu itathawa kuyankha mafunso ku nkumano omwe inakonza ku Lilongwe.

Atangomaliza kulakhula Kwa atolankhani, a Chithyola anatuluka mwachangu achitetezo ali m’mbalimu.

Atolankhani ambiri adandaula kuti sikumayenera kutero chifukwa ndunayi inayitanitsa msonkhano wa atolankhani ndipo kufunsidwa mafunso ndi gawo limodz la msonkhanowu.

Pa nkumanowu ndunayi yalengeza ndondomoke zomwe ayike kuti zithandize a Malawi pa nthawi yowawitsayi.

Zina mwa ndondomeko zimene nduna yachuma Simplex Chithyola Banda yalengeza ndi yoti aMalawi 184,920 omwe anakhudzidwa ndi Cyclone Freddy adzilandira K50,000 pamwezi kwa miyezi itatu. Mabanja 105,000 a mtauni alandira K150,000.

A Chithyola atinso boma kudzera mwa apolisi lithana ndi aliyense ogulitsa ndalama za maiko akunja mosavomerezeka

Malingana ndi a Chithyola, boma lithananso ndi anthu ogwira ntchito m’mabanki omwe akuti amatenga ndalama za kunja kuchoka mumabanki kukagulitsa pa misika yosavomerezeka.

Izi zikudza pamene boma latsitsa ndalama ya Kwacha ndi ma pelesenti 44 zomwe zapangitsa kuti mitengo ya zinthu izikwere.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.