Malawi yakumbukira asilikali omwe adamenya nawo nkhondo za dziko lapansi

Advertisement
Saulos Chilima Remembrance Day

Mwambo okumbukira asilikali omwe adamenya nkhondo ya dziko lonse lapansi udachitika lero ku chipilala chachikumbutso ku Cobbe Barracks ku Zomba.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Saulos Chilima ndi yemwe adatsogolera mtundu wa a Malawi panwambowo.

A Chilima adafika kumwambowo pomwe nthawi imangokwana 10:58 mamawa ndipo adayala nkhata yamaluwa pachipilala chachikumbutsochocho.

Kuno ku Malawi mwambowu umachitika pa 11 November kapena Lamulungu lachiwiri wa Mwezi wa November chaka  chilichonse nthawi ya 11 koloko.

Ena omwe adayala nkhata zamaluwa ndi mkulu wa asilikari ankhodo General Paul Velentino Phiri, mkulu wa apolisi m’dziko muno Inspector General Merlyne Yolamu, Sipikila wakunyumba yamalamulo Catherine Gotani Hara, mkulu wa oweruza milandu mdziko muno Justice Rizine Mzikamanda, mtsogoleri wa zipani zotsutsa Boma kunyumba yamalamulo a Kondwani Nankhumwa, akezembe a maiko a Japan ndi Tanzania, mkulu wa bungwe la Red Cross mdziko muno, kungotchulapo ochepa.

Mwambo ngati omweu udachitikanso ku Lilongwe mchigawo chapakati ndipo udatsogoleredwa ndi a Harry Mkandawire ndipo mwambo winanso udachitika mu mzinda wa Mzuzu mchigawo chakumpoto ndipo adatsogolera ndi a Michael Usi omwe ndi Nduna ya za chilengedwe.

Advertisement