Ndine okwiya kwambiri, mudzayankha mukundipangazi – walira mokweza Norman Chisale

Advertisement
Norman Chisale former presidential bodyguard

…wati anthu akuzuzika kwambiri pano kusiyana ndi nthawi ya DPP

…wati sadzawakhululukira a Steven Kayuni

Wachitetezo wamkulu wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Peter Mutharika, a Norman Paulos Chisale sanafuna kusunga zakukhosi pomwe awulura kuti akuzunzika kaamba ka ndale ndipo ati onse omwe akuwazuza pano, ayembekeze kudzayankha kutsogoloku.

A Chisale omwe pano ali ndi zaka 42 ndipo amachokera m’boma la Ntcheu, amayankhula izi lolemba pa 6 October, 2023 kudzera mu pologalamu ya padera yomwe inajambulidwa ndikuwulutsidwa pa wailesi ya Zodiak.

Mkuluyu yemwe unyolo unalephera kukata mmanja mwake makamaka m’chaka cha 2020 pomwe boma la mgwirizano wa Tonse linatenga ulamuliro, sanapsatile chichewa za mafunde a mazuzo komaso mikwingwilima yomwe moyo wake ukudutsa pakadali pano.

Mikwingwilimayi ikubwera kamba koti ma bizinezi awo alowa pansi komaso kamba koti khothi linatseka kaye ma akaunti yawo yabanki zomwe akuti zikuwapangitsa kukanika kuchita zinthu zina kuphatikiza kusowa ndalama yothandizira banja lawo pamodzi ndi azibale awo ndipo ati pano akufuna achotse ntchito ena mwa anthu omwe amamugwilira ntchito.

“Ndimayeselayesela kupanga mabizinezi koma palibe bizinezi iliyose yomwe ndinganene kuti ikuyenda pano. Ndili pano ndinganene kuti mwina mawa ndikhala ndikuchotsa anthu ntchito okwana 12 kuti ayi basi kapumeni sindikwanitsa,” anatelo Chisale.

Mkuluyu anapitilira kuwulura kuti pano ndiwokwiya kwambiri kamba ka kumangidwa kwambirimbiri komwe wakhala akumangidwa ndipo wanenetsa kuti milandu yambiri yomwe amamumangira ndiya bodza komaso ndi kamba ka ndale chabe.

Apa mopsa mtima kwinaku akumenya tebulo, a Chisale anatchula nduna yawona za chilungamo a Titus Mvalo kuti ndi m’modzi mwa anthu omwe akuwazuza iwo pa zifukwa zandale ndipo ati zomwe akupangazo sizabwino.

A Chisale anapitilira ndikudzudzula apolisi chifukwa cholephera kutsata malamulo pomwe iwo amamangidwa ponena kuti ankayenera kumangidwa kamodzi kenaka ndikuwawunjikira milandu yose yomwe akuganizilidwa osati zomwe zinkachitika zoti akangotuluka ku polisi pa belo, mkukwingidzidwaso.

Apa mkuluyu m’maso muli gwaa wawopseza kuti onse omwe akumuzuza pano komaso apolisi omwe anaphwanya malamulo pakumangidwa kwake, ayembekezele mbonawona pomwe wati ayankha milandu yawo posachedwapa.

“Munthune ndine okwiya kwambiri. Nane ndine munthu, ndakhala ndikumangidwa kambirimbiri. Kumangidwa komwe ndinamangidwa ine, kunena zoona anthu adzayankha ngakhale nditakhala kuti ndamwalira; wina adzabwera mkufuna kuwona chilungamo kuti nchifukwa chiyani ndinamangidwa mwa chonchi? Lamulo limati tengani milandu yose kampatseni munthu mukamumanga osati zomwe amachitazi zomati ndikamatuluka ku polisi kundimanga.

“Pankhani ya kalata yomwe ndinalemba, choyamba ndinene kuti sindinaone nduna ya bodza ngati imene ija. Minister of justice amayenera kukhala munthu wachilungamo. Ndinakapeleka ndekha kalata pamanja, lero chiminisitacho chidzikati sichinalandile kalata zowona? Zimenezo mzopusa, ndikuva kuwawa, nane ndine munthu.

“Ndikuvutika chifukwa cha ndale pamene ine sindipanga ndalezo. Ndipo ndikubwereza nduna ya zachilungamo akundizuza chifukwa cha ndale ndipo ndili ndi umboni. Abwere poyera a Mvalo-wo kuti ndiwauze kuti akundizuza chifukwa cha ndale,” anateloso Chisale.

Mu pologalamu yomweyi, Chisale wanenetsa kuti sadzawakhulukira oyimilira boma pa milandu opuma Steven Kayuni ponena kuti ndimunthu m’modzi amene anawonjezera makala pakuvutika kwawo ndipo ati anali odabwa kuti a Kayuni anawaimbira foni posachedwapa kuwapepesa.

Podziwa kuti odya nyemba amaiwala koma otaya makoko samayiwala, mkuluyu wati ngakhale a Kayuni anapepesa, koma iwo sadzawakhululukira mpaka kalekale ponena kuti samaiwala zomwe anawachita kuphatikiza kukana kuti atenge ndalama ina ku banki yawo yomwe inatsekedwa kaye kuti akalipilire mwana sukulu pa nthawi yomwe iwo anali nchitokosi.

“Ndili ku polisi ndinapempha kuti atenge 3 miliyoni kwacha ku akaunti yanga amulipilire mwana sukulu fizi, koma a Steven Kayuni anakana. Ndipo a Kayuni kumene muliko Mulungu akukhululukileni. Munazuza ine, banja langa komaso azibale anga, tsiku limodzi chilungamo chidzaoneka.

“Ndiwauze a Malawi kuti a Steven Kayuni ndakana kuwakhululukira. Ndinayankhula nawo pa foni kudzera kwa munthu wina wa MCP kundipepesa kuti anandilakwira ndipo anati ali okozeka kuthandizira kuti ndipeze chilungamo. Ndipo ndili ndi umboni zomwe ndikunenazi, ngati ndikunama iwowo abwere poyera atsutse. Mulungu achite nawo a Kayuni koma ine sindingakhululuke zomwe anachita,” wanenetsa Chisale.

Poyankhula za momwe dziko lino likuyendera, Chisale wati a Malawi ambiri akuzuzika kwambiri pano kuyelekeza ndi nthawi yomwe chipani cha DPP chinali pachiongolero ndipo wati Peter Mutharika ndi yemwe ali ndikuthekera kotulutsa dziko lino m’mavuto omwe likudutsa.

 “Kuzuzika kwa anthu nthawi ino ndi nthawi ya DPP ndizosiyana, anthu atha kukhala kuti amazuzika nthawi imene ija koma ndalama komaso chakudya amazipeza. Ndi kwa bwino APM ayime kuti apulumutse a Malawi amene akuvutikawa,” anateloso.

Chisale anakambaso nkhani ya kupezeka kwa amwenye m’dziko muno omwe wati nawo sakuyenera kumazuzika kamba koti nawoso dziko lino ndi lawo.

A Paulos Chisale anapitilira ndi kunena kuti chuma chomwe ali nacho pano anachipeza asanakhale wachitetezo wa Peter Mutharika ndipo wati amadabwa kwambiri anthu akamawanena kuti chumachi anachipeza munjira zosayenera.

Apa anafotokoza kuti anthu ambiri omwe ali m’boma lero, wawapatsapo thandizo m’mbuyomu nthawi imeneyo asanaloweso ndipo ati anali nsilikali oyambilira kugula selefoni (cellphone) ku Malawi Defense Force ndipo watchalenja kuti amene akuona kuti a Chisale-wo anapanga katangale, apite akawanenele ndikupeleka umboni wawo ku ACB.

Advertisement