U-Doc uja wapita basi? UNISA yati siinapeleke madigili aulemu kwa Namadingo, Mphande

Advertisement
Patience Namadingo

Zikuoneka kuti madobadoba aku Nigeria komaso matsotsi aku South Africa athira mchenga mumpunga wagulu pomwe awonetsa Pemphero Mphande ndi Patience Namadingo chidameta nkhanga mpala powapatsa ma digili awulemu abodza.

Chatsitsa dzaye nchakuti kuyambira lamulungu sabata ino, dzina la Pemphero Mphande linali posepose pomwe anauza mtundu wa a Malawi kuti atha kumatchedwano dokotala kamba koti sukulu ya ukachenjede ya South Africa (UNISA), yawaninkha digili yaulemu.

Koma nkhaniyi inakali mkamwamkamwa, sukulu ya UNISA yabwera poyera ndikutsutsa mwantu wagalu kuti iyo siyinapeleke ma digili aulemu kwa Mphande yemwe anthu pomunyadira amangoti ‘Mr P’, oyimba Patience Namadingo komaso Sharif Karim.

UNISA kudzera munchikalata chomwe yatulutsa lachiwiri pa 7 November, 2023, yakanitsitsa mwantu wagalu kuti siyinapeleke ma digili aulemu kwa mphangala zitatuzi ndipo sukuluyi yati inamva za nkhaniyi kudzera m’masamba anchezo.

“Univesite ya South Africa (UNISA) yazindikira kudzera m’manyuzipepala ndi m’manyuzipepala kuti m’Malawi Phemphero Mphande, woyimba ku Malawi Patience Namadingo komanso munthu wina dzina lake Mansoor Sharif Karim akuti adalandira digiri ya udokotala ku yunivesiteyi mu 2020. 2022 ndi 2023 motsatana.

“UNISA ikufuna kunena mosapita m’mbali kuti SINAPATSE madigirii aliwonse oterowo pa atatuwa komanso kuti zonena za izi SIZOONA. Anthu atatuwa salinso m’gulu la osankhidwa omwe amaganiziridwa ndikuvomerezedwa kuti apatsidwe ma digili olemekezeka mu 2020, 2021 ndi 2023. Komanso sanasankhidwepo, kuganiziridwa kapena kuvomerezedwa kuti adzalandire ulemu woterewu nthawi ina iliyonse. Palibe madigiri aulemu omwe adaperekedwa mu 2022,” yatero UNISA.

Kuphatikiza apo, sukuluyi yati zikalata zaulemu (certificate) zomwe Mphande komaso Namadingo anawonetsa a Malawi, sizomwe sukulu ya UNISA imapeleka kwa anthu omwe achita bwino pa maphunziro kapena m’moyo uno.

Sukuluyi yatiso kuperekedwa kwa ma digili aulemu ku UNISA kumachitika kudzera mnjira yoyendetsedwa bwino, ndipo yati kusankha ndi kuvomereza kumayendetsedwa ndi nthambi zosiyanasiyana za sukuluyo mpaka kuvomerezedwa komaliza ndi University Council.

Pakadali pano sukuluyi yati yauza akatswiri ena pasukuluyi kuti afufuze bwino bwino za nkhaniyi ndipo yati ikupanga zoti anthu atatuwa asiye kutchula sukuluyi pa madigili aulemu omwe akunenedwawo.

“Ife ngati yunivesite, tikudzitalikitsa ku nkhani zabodzazi komanso tikudzudzula mwamphamvu kugwiritsa ntchito molakwika dzina la UNISA pakuchita zachinyengo. Akuluakulu asukuluyi awuzidwa kuti awunike nkhaniyi ndikuonetsetsa kuti anthuwa afusidwe komaso asiye kunena zonamazo,” watelo ogwirizira udindo wa wamkulu wa sukuluyi Professor Moloko Sepota

Advertisement