Chakwera apita ku Saudi Arabia ndi Egypt ndi anthu osachepera 70

Advertisement
President Lazarus Chakwera in a plane

Boma lati mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ayenda ndi anthu osachepera 70 paulendo wake opita ku mayiko a Saudi Arabia komanso Egypt womwe anyamuke mawa lachitatu.

Malingana ndi nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu, a Chakwera akuyembekezeka kukakhala nawo pa chiwonetsero cha malonda chomwe chikutchedwa Egypt Intra-Africa Trade Fair.

A Kunkuyu ati ku Saudi Arabia, a Chakwera akakhala nawo pa nsokhano wa mayiko aku Africa ndiso ku Arab omwe ukutchedwa Africa-Arab Summit.

A Kunkuyu omwe amayankhula lero pa nsonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe wati maulendo awiriwa ndiofunika kwambiri makamaka ku mbali nkhani yokweza chuma cha dziko lino.

Malingana ndi ndunayi, ku Saudi Arabia Pulezidenti Chakwera akakumana ndi akatakwe pa ntchito za malonda omwe akakambirane nawo zokhudza nkhani za ulimi, malonda komanso nthambi zina zosiyanasiyana za chitukuko.

A Kunkuyu at anthu osachepera 70 ndi omwe apite nawo paulendo wa a Chakwera ndipo ati ambiri mwa anthuwa ndi nthumwi za makampani osiyanasiyana m’dziko muno.

Apa iwo anati ma kampaniwa omwe atumiza nthumwi ku maulendo onsewa, apeleka kale ndalama zothadizira paulendowu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.