…wati timu yomwe ingamufune ku Malawi ilimbe mthumba
Mphangala yosewera mpira wa miyendo Khuda ‘Ikena’ Myaba wati iye ndamene wathetsa mgwirizano ndi timu ya Tishreen SC ya ku Syria kamba koti siyimamupatsa makobidi ndipo wati atha kusewera ku mpanje kuno ngati timu yomwe imufune ingakwanitse kumulipira.
Myaba yemwe anapita ku timu ya Tishreen SC mwezi wa August chaka chino, amayankhula izi kutsatira mphekesera zomwe zakhala zikumveka kuti timuyi ndi yomwe yamubudura kamba koti katswiriyu walowa pansi maseweredwe ake.
Mu kanema yemwe watulutsa, Myaba yemwe m’mbuyomu anali osewera odalilika ku tsogolo kwa timu yayikulu ya dziko lino, wati chiyambileni kusewera mpira ku timuyi, wapatsidwa ndalama mwezi umodzi okha zomwe a kuti ndizovuta potengera kuti iye ndi munthu wa pa banja.
Osewerayu waulura kuti iye kudzera mwa omuyimilira ake anapempha timu ya Tishreen SC kuti ithetse mgwirizano wake zomwe zachitika mkati mwa sabata yatha ndipo a kuti pano ndionyadira tsopano.
“Anthu ambiri akusangalala kuti achita bwino kumuchotsa timu, ndikufuna nditsutse pamenepo, ine timu sindimachotsedwa, ndimachoka ndekha. Ndathetsa mgwirizano chifukwa timu siyimakwanitsa kundilipira salale. Timu ilibe oyithandiza ndipo imanena kuti itha kumandilipira ine pa nthawi yomwe yapeza ndalama zomwe ineyo sindingakwanitse.
“Ndakhalako miyezi atatu ndipo pamiyezi imeneyo anandilipira mwezi umodzi okha amati ndalama alibe ndipo siine ndekha. Osewera ambiri timuyi ili nawo ngongole. Nde m’mene ndimazionera ineyo sindimayenera ku mamenya timu imeneyo iyayi ndipo ndimadandaula kuti nchifukwa chiyani ndinapita ku Syria kumakasewelera timu ngati imeneyo,” anatelo Myaba.
Pakadali pano katswiriyu wati atha kubwera kudzasewera mpira wake kuno ku mudzi pokhapokha papezeke kaye timu yomwe ingawonetse chidwi choti itha kukwanitsa kumulipira ndalama zomwe akufuna.
Mphangalayi yati iyo imakonda ndalama ndipo yati imatengedwa yopanda khalidwe chifukwa choti nthawi zonse imafuna chilungamo chiyende ngati madzi.
“Ngati matimu ena ku Malawi ilipo omwe akunena kuti akwanitsa kundilipira salale yomwe ndikufuna komaso kundipatsa signing on fee, ndiwasewelera chifukwa choti kwa ine mpira ndi business ndipo ine ndimakonda ndalama. Sindingamapite ku timu koti anandilonjeza kuti adzindipatsa 4 miliyoni Kwacha nde nkumandiuza kuti sandipatsa ndalamayo, sizingatheke. Nde ndi bwino kukhala osewera opanda khalidwe koma wachilungamo. Ine ndimatsogoza chilungamo,” anawonjezera choncho Myaba.
Osewerayu wadzudzula a Malawi ena omwe a kuti amakondwera mzawo zikamamuvuta ponena kuti anthu ambiri atamva kuti iye wachoka ku timu ya Tishreen SC, anasangala poganiza kuti osewelayu wapwetekedwa basi, koma watsindika kuti iye inakali ndi nthanana ndipo sakuvutika.
Asanapite ku Syria, Myaba anali m’dziko la South Africa komwe amasewelera timu ya Polokwane City ndipo mu miyezi iwiri yomwe katswiriyu wakhala akusewelera ku Timuyi Tishreen SC, wagolesa zigoli zinayi mumasewero atatu ndipo wathandizira kawiri konse popezesa mwayi kuti anzake apeze zigoli.