Mankhwala a chifuwa chachikulu cha TB ndi aulere – atero adindo

Advertisement
HIV and AIDS expert from National Tuberculosis and Leprosy Elimination Programme (NTLEP) Dr Samuel Chirwa

Mpakana pano, anthu ena amaona ngati mankhwala amatenda a chifuwa chachikulu cha TB ndi ogulitsa zinthu zomwe adindo ati zakhala zikupangitsa ena mwa anthu odwala matendawa kuti asamalandire mankhwala mwandondomeko yoyenera komanso kusapita kolandira mankhwala kumene.

Izi zadziwika pamene bungwe la African Institute for Development Policy (AFIDEP) mogwirizana ndi bungwe la Journalists Association Against AIDS ndi mabungwe ena adapangitsa msonkhano lachinayi mu Mzinda wa Lilongwe.

Poyankhulapo, Katswiri wa Matenda a Chifuwa  Chachikulu komanso HIV and AIDS kuchokera ku Bungwe la National Tuberculosis and Leprosy Elimination Programme (NTLEP) Dr Samuel Chirwa anati pakufunika ndondomeko yoyenera yoti anthu dziko muno adziwe kuti Mankhwala amatenda a chifuwa chachikulu cha TB ndi aulere kuchipatala konse kumene mankhwalawa amapedzeka.

A Chirwa anatinso anthu akuyeneranso kudziwa kuti  Nthendayi ndiyochizika ngati odwala wamwa mankhwala mwandondomeko yoyenera.

“Potengera kafukufuku wathu, tikuchita bwino ndithu kutengera m’mene tinalili mchaka Cha 2015. TB yakhala ikusintha chaka chilichonse potengera ndi m’mene imapedzekera. Izi zikuonetsa kuti anthu akudziwa za nthendayi,” adafotokoza motero.

Poyankhulapo, wopanga kafukufuku ku bungwe la AFIDEP Dr Benjamin Azariah Mosiwa wati kafukufuku amene anapanga akusonyeza kuti abambo  ndi omwe akumanyalanyaza kupita ku chipatala kukayezetsa ngakhalenso kumwa mankhwala mwandondomeko yoyenera ndipo ati iwo ngati bungwe achitapo kanthu.

A Rhoda Mbeta omwe anapezeka ndi nthenda ya TB mchaka cha 2010 anati kale nkhani ya nthendayi idali yovuta chifukwa cha mchitidwe osalidwa omwe unalipo pamene munthu wapezeka ndi nthendayi komano pano anthu atadzindikira zinthu zinasintha.

A Mbeta omwe pano anachira ku nthendayi, adafotokoza kuti atapezeka ndi nthendayi adagonekedwa mchipatala kwa miyezi itatu ndipo panalibe yemwe adawaonapo kuchipatala ngakhale achibale chifukwa chosalidwa komano pano amatha kuchza ndi anthu bwinobwino opanda vuto lilonse.

Advertisement