Bambo amulamula kukakhala ku ndende zaka 11 chifukwa chogwilirira mwana

Advertisement

Bwalo la milandu ku Liwonde mu boma la Machinga lalamula bambo wina wa zaka 27 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndikukagwila ukaidi wakalavula gaga kwa zaka 11 chifukwa chopezeka olakwa pamulandu ogwirilira mwana wa zaka 14.

Mkulu wa a Police Boma la Machinga Deputy Commissioner Jane Mandala watsimikiza zankhaniyi poyankhula ndi Malawi24.

Deputy Commissioner Mandala wati wapolisi woyimira boma pamilandu Sergeant Gift Kalamula adawuza bwalo kuti apereke chilango chokhwima kwa a Kapachika chifukwa milandu yogonana ndi ana ikuchulukirachulukira m’dziko muno choncho anthu ena atengerepo phunziro

Mu bwalo lamilandu, a George Kapachika adawuvomera mulanduwo ndipo adapempha bwalo kuti lisawapatse chilango chokhwima popeza kupalamulaku kudali koyamba komanso ali ndi banja lomwe amaliyang’anira.

Koma popereka chigamulo chake, First Grade Magistrate Lawrence Mangani adagwirizana ndiwapolisi oyimira boma pamilandu kuti milandu yogwirilira ana ikuchulukira m’dziko muno choncho ndipofunika kuti apereke chilango chokhwima kuti abambo ena atengerepo phunziro. Pamenepa adalamula kuti George Kapachika akakhale kundende ndikukagwira ukaidi wakalavula gaga kwa zaka 11.

George Kapachika ndiwa zaka 27 zakubadwa ndipo amachokera mudzi mwa Tchokola, T/A Kumtumanje Boma la Zomba.

Advertisement