Chakula chinkulirano pakati pa oyimba wa makono ndi wina wamvula zakale, ndipo zili ngati dzana likumenyana ndi mawa pomwe JB akuponyerana zibonyongo ndi K Banton; mwanayo akadzati unakwatira nkhalamba, wankuluyo koma chiphuzo cha kuno ndi ukoo. Awawa aleletseni apwetekana.
Oyimba Khumbo Storrah otchedwa K Banton ndi oyimba nzake Alberto Fernando Zacharias otchedwa Jolly Bro mwachidule JB, aponyera kaye uko magitala ndi zingw’enyengw’enye zina pomwe atengetsana chulu chatchula pa fesibuku.
Mkangano wa awiriwa wayamba pomwe K Banton posachedwapa anauza kanema ya Podcast Malawi kuti iyeyu ali mwana cha m’ma 2009 anatetezapo JB pomwe ankafuna kumenyedwa ndi oyimba nzake Phyzix munzinda wa Blantyre.
Izi zinakwiyitsa JB ndipo monga mwa chikhalidwe chaka anayamba kumubongetsa mwanayu kudzera pa tsamba lake la fesibuku ndipo wakhala akumunyoza K Banton ndipo mwa zina wakhala akumunena kuti ndi “nkaladi onunkhira zikanga.”
“Achimwene che K Bandatoni uluya ndi maluzi sizigwirizana. Izi zongowezuka opanda ndalamazi ndi danger. Kuyela kumafunika dollar. Masikini akakhala wachikaladi m’malo mokuti anthu athandize amamuseka. Za nyimbo tayikani kaye pambali, pezani ka ganyu penapake muzigobola, mukuonekela ng’ambatu. Chifukwa nde umphawi wakunyapulatu bwanawe.
“Achina bandatoni akaladi aku nkhamenya odzola fair and lovely asanagone,” analemba choncho JB pa fesibuku m’mauthenga ake awiri osiyana.
Chinkuliranochi chinafika pa mponda chimera kumathero asabata yangothayi ndipo masamba a oyimba awiriwa anali teketeke pomwe anthu amati akaikira mlomo kwa JB, amathamangiraso kwa KB kukaipatsa moto.
Chatsitsa dzaye nchakuti loweruka lapitali K Banton analowa layivi (live) pa tsamba lake la fesibuku pomwe anamusambwadza JB yemwe pano akukhala m’dziko la America.
Oyimba waku Machinjiri-yu, anamubayira JB kuti anakwatira nkhalamba ndipo mawu awa anatokosola nkwiyo wa nzakeyu yemwe naye anayamba kulavula makala a moto kwinaku akumutchura KB za nkabudura.
“Ataisambitsa nkhalambayo kwa zaka zitatu anangoganiza zoyikwatira,” anatelo K Banton mu uthenga omwe unakwiyitsa Jolly Bro.
Poyankha zomwe anayankhula KB, JB anavumbulutsa maphuzo pa nzakeyu kuphatikiza kutukwana makolo a nzakeyo ponena kuti samayenera kumunyozera nyenyezi yake ya chizunguyo.
“Iwe K Bandatoni ndizabwino bwino kugemulana iwe ndi ine koma kumanyoza nkazi wanga okuti sizikumukhuza nde ndimadana nazo. Pa chifukwa chimenecho pa n*o pa mako wanva ukasume,” anayankha choncho JB.
Anthu ena omwe akuyikira ndemanga za nkhaniyi, ati ndizodandaulitsa kuti kusavana kwa awiriwa kwafika mlingo uwu.