Chakwera wapeleka puloti, K1.5 miliyoni kwa osewera aliyese wa Scorchers

Advertisement
Malawi Women's National Football Team have been congratulated by President Lazarus Chakwera

Asungwana osewera mpira wa miyendo mu timu ya dziko lino ya Scorchers, akusimba lokoma pomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati apereka 1.5 million kwacha komanso malo omangapo nyumba kwa osewera aliyese.

Chakwera walengeza za nkhaniyi lero lachitatu ku nyumba ya boma ya Kamuzu munzinda Lilongwe komwe anakonzera nkhomaliro osewera atimu ya Scorchers pokondwelera kuti timuyi yatenga chikho cha COSAFA.

M’mawu ake mtsogoleri wa dziko linoyu wati ndikofunika kwambiri kuyamikira zomwe achita atsikana ododa chikopawa pobweretsa chimwemwe ku mtundu wa Malawi.

Apa a Chakwera alonjeza kuti apeleka kwa msungwana aliyense wa timu ya Scorchers malo omanga nyumba ku Area 45 mu mzinda wa Lilongwe omwe ndi okula malipande 35 mulitali ndi 25 mulifupi.

Pomwe osewerawa amawona ngati zathera pompo, Chakwera anawonjezera kuti apelekaso ndalama yokwana 1.5 miliyoni kwacha kwa osewera onse omwe anatenga nawo gawo ku mpikisano wa COSAFA.

Tate wa dzikoyu walangizaso ma kampani ndi mabungwe m’dziko muno kuti amene angakwanitse kutelo apeleke mphatso kwa osewerawa zomwe a kuti ziwalimbikitsa kuti azachiteso bwino mmipikisano ina.

Timu ya dziko linoyi inatenga chikho mumpikisano wa COSAFA itagonjetsa timu ya Zambia ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi komaso siyinagonjenso mmasewero ake onse asanu.

Advertisement