A Chakwera akupita ku Mozambique mawa

Advertisement
Malawi President Lazarus Chakwera

Patangotha masiku ochepa chibwelereni kuchokera ku Amerika, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera mawa anyamuka kupita ku Mozambique.

A Chakwera anyamuka ku Mozambique mawa ndipo akabwerako tsiku lomwelo.

Malingana ndi nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu, a Chakwera ku Mozambique akakumana ndi mtsogoleri wa dzikolo a Felipe Nyusi komanso mtsogoleri wa dziko la Zambia a Hakainde Hichilema.

A Kunkuyu anaonjezera kunena kuti atsogoleri atatuwa akakambilananso za kusowa kwa mafuta agalimoto komanso za doko la Nacala.

Iwo akuti boma likukhulupirira kuti vuto la mafuta lomwe lili kuno ku Malawi litha kukonzedwa msanga pogwiritsa ntchito doko la Nacala.

Mu mwezi wa Sepitambala pa 15, a Chakwera anatulukanso mdziko lino kupita ku Amerika komwe anakakhalako masiku 17 ndipo abwera lolemba lapitali pa 2 Okotobala.

Advertisement